MPHAMVU YA NYIMBO ZÀ KU MALAWI
Nyimbo ndi chinthu chimodzi chimene chimapezeka mnyengo zonse za munthu. Mkulu wa bungwe loyanga’anira oyimba mdziko muno la Musicians Union of Malawi ,Vita Chirwa, akufotokoza za momwe mayimbidwe akuyendera. “Maimbidwe kuno kwathu ku Malawi, akupita patsogolo. Taona oyimba kuno kwathu akuitanidwa kupita kukayimba ku Mayiko akunja komanso kuwina photho za padziko lonse”. Vita wayamikira atsogoleri […]

UBWINO WA KUKONZEKERA POCHITA ZINTHU.
Pamene mumatsegula tsambali kuti muwerenge nkhaniyi ,ndiri nacho chikhulupiriro kuti munakonzekera.Munthu umakhala kakasi kapena kusowa mtengo ogwira ngati sunakonzekere pakuchita chinachake.Mbusa Vincent Nguluwe, watambasula kukonzekera kuti ndi kukonzekera zinthu zomwe munthu ukufuna kuti uchite kuti ukafikire china chake. “Kukonzikera kudayamba ndi Mulungu. Genesis 1 ndime ya 1″. Watero , Nguluwe. Mbusayu, wati kukonzekera kumathandizira munthu […]

CHIMWEMWE MU ULIMI WA MITENGO
Zolemba zambiri zimafotokoza kuti ulimi ndi kudzala mbewu komanso kuweta zifuyo pa Malo ogwiritsidwa ntchito ndi anthu. Mutha kututumuka mutamva kuti ulimi ndi kudzala mbewu, kuweta Nyama ndi kubzala mitengo, pozisamalira ndi kuikolola. Musatutumuke ndi zomwe mwamvazi popeza izi ndi zochitika ndithu. Mkulu wa kampani ya Headman Nursery , Elijah Nyirenda ochokera ku Nkhatabay, wafotokoza […]

PHINDU LA MAPHUNZIRO A CHUMA KU MALAWI
Chuma ndi chinthu chimene chimafunikira kwambiri pa moyo wa munthu aliyense posatengera komwe munthu amachokera. Maphunziro a nkhani za chuma kuno kwathu ndi mnyanga wa njobvu. Katswiri pa nkhani ya zachuma,Innocent Banda watsindika kuti muli phindu mma phunziro a nkhani za chuma”Maphunziro a zachuma ali ndi phindu pa munthu payekha chifukwa Ndalama-zo amazipeza ndi munthu”. […]
