Chuma ndi chinthu chimene chimafunikira kwambiri pa moyo wa munthu aliyense posatengera komwe munthu amachokera. Maphunziro a nkhani za chuma kuno kwathu ndi mnyanga wa njobvu. Katswiri pa nkhani ya zachuma,Innocent Banda watsindika kuti muli phindu mma phunziro a nkhani za chuma”Maphunziro a zachuma ali ndi phindu pa munthu payekha chifukwa Ndalama-zo amazipeza ndi munthu”. […]