Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

ACHINYAMATA APATSIDWE MPATA OTSOGOLERA DZIKO

Written by on August 18, 2024

Nzosabisa kuti kwa nthawi yaitali achinyamata amauzidwa kuti ndi atsogoleri a mawa ,koma izi siziri chomwechi popeza katswiri pa Ndale mdziko muno a George Phiri, wati achinyamata ndi atsogoleri a lero.”Achinyamata tisamawanamize kuti adzakhala atsogoleri a mawa ayi. Tiyeni tisinthe ka ganizidwe ndipo ndibwino kuti achinyamta-wa apatsidwe mpata otsogolera lero. Wachinyamata ndi wachinyamata lero”.

Malingana ndi Katwsiriyu, kuyambira Mchaka cha 1964 kufikira lero(2024), achinyamata akugwiritsidwa ntchito molakwika monga kutumidwa ndi atsogoleri a Ndale kuti azimenya anthu osiyana nawo zipani mmalo momawakonzekeretsa kumapanga nawo ziganizo zoyendetsera dziko lino.

A Phiri ati, wachinyamata amene ali ndi zaka makumi atatu ndi Mphambu zisanu (35), asadziyang’anire pansi koma kutenga nawo gawo kuti atha kupanga ziganizo zoyenerera ngakhalenso kutsogolera dziko.

Kumbali ya Chikhalidwe, a Phiri anena kuti kunjaku kuli zikhalidwe zosiyanasiyana koma pamayenera kukhala Chikhalidwe chomwe Mtsogoleri amayenera kukhalamo. Iye wapempha achinyamata kuti asatengeke ndi zikhalidwe zina ngati Chikhalidwe cha Nkhanza, Kutukwana ndi kuonera zinthu zotsutsana ndi Chikhalidwe cha chiMalawi.

George Phiri , wafotokoza kuti wachinyamata ozindikira amayenera kukhala odziwa kusiyanitsa Chikhalidwe cha a Malawi choyenera ndi choyipa, zikhalidwe za anthu a mmaiko ena komanso amakhala wophunzira.

“Achinyamata ali ndi ntchito yodzinola kuti akhale mu Chikhalidwe chodzilemekeza. Umunthu umagwirizana ndi Chikhalidwe. Kotero kuti, Umunthu umathandiza kudziwa kuti ndiri nawowa ndi anthu oti akumva zomwe inenso ndikhonza kumva, zokoma ngakhale zowawa. Umunthu umathandiza kuti zokoma zomwe ukufuna,enanso umawafunira zomwezo”. Iye anatero.

Posachedwapa Chipani cha Malawi Congress, chidakatenga chiletso ku bwalo la Milandu mu Mzinda wa Lilongwe, Kuletsa anthu omwe ndi achinyamata omwe sadatumikire Chipani-chi kwa zaka ziwiri, sakuyera kutenga nawo gawo popikisana ndi mkhalakale pa Ndale pa Msonkhano wake wa ukulu osankha adindo a Chipani.


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist