KAUNIUNI WA MOYO AZICHITIKA NDITHU PA MALAWI
Written by Kradio on October 13, 2024
Galimoto za mtidzi, nyumba za pamwamba komanso zovala zodula ndi zina mwa zinthu zomwe mtima umafuna utazipeza mmoyowu.Ichi chifukwa chake pali mkuluwiko wotchedwa ‘mtima Suvala Sanza’.
Davis Damison yemwe ndi mkulu wa Community Initiative for Social Empowerment (CISE)Malawi , wafotokoza kuti kauniuni wa Moyo (life style audit)ndi makhalidwe a munthu potengera zinthu zimene wapeza kapena kutaya.
Damison wati mbiri ya Ndale ndi utsogoleri mdziko muno imati yemwe adali Mtsogoleri woyamba wa dziko lino Malemu Dr. Hastings Kamuzu Banda ,adali yekhayo amene ankachita kauniuni munthu akafuna kupanga chitukuko.”Dr Hastings Kamuzu Banda, adali patsogolo kupanga kauniuni kwa munthu aliyense (wogwira ntchito m’boma olo Malonda)akafuna kumanga Nyumba yapamwamba. Chimene amapanga amafunsidwa munthu uja kuti Ndalama wazitenga kuti ,ukupanga Malonda anji,umagwira ntchito yanji?”. Iye, wati izi zimathandizira kuti munthu akhale ndi popezera ndalama pogwirika.
Mkulu waku CISE Malawi-yu, wati ndizodandaulitsa kuti munthu amasintha momwe amakhalira akapatsidwa udindo m’boma kapena ku Chipani. “Anthu amakhala ndi nkhawa anthu a akapatsidwa ma udindo ndipo anthu sangapeze mayankho kaamba ka mphanvu zimene adindo amakhala nazo, makhalidwe akasintha ndipo ndi ntchito yofunika kafukufuku”.
Damison wati kupanga kauniuni nkofunikira kwa munthu pa iye yekha ngakhale Boma popeza kumapereka chiyembekezo kwa anthu komanso ku Boma. Anthu amakhala ndi chikhulupiliro kuti palibe amene akusakaza misonkho.
Kumbali yothana ndi katangale ndi Ziphuphu Davis Damison wanena poyera kuti Boma la Mgwirizano wa Tonse sirinayike patsogolo chidwi chothana ndi katangale.” A Malawi siwokhutira mmene Bomali likupangira pa nkhani ya Katangale chifukwa pali milandu yambirimbiri imene a Malawi amaitsatira .Chiyembekezo chawo chinali chokut enieni akupanga katangale azengedwe milandu,chilango chiperekedwe pofuna kupereka phunziro kwa a Malawi ena”. Damison ,watero.Komabe Iye wachita changu kunena kuti ngati Boma pali zinthu zingapo zofuna kuthana ndi katangale. Iye watchulapo ndondomeko monga kutsegulidwa kwa ofesi ya bungwe la ACB m’boma la Mchinji.
Iye, wati atsogoleri ambiri amabwezedwa mbuyo posafuna kusakhala ndi makhalidwe abwino chifukwa adindo ambiri ali ndi moyo odziwonetsera pa zinthu zimene alinazo. Mwachitsanzo, kukhala ndi gulu lotchedwa ma ‘big men’. Malingana ndi a Damison, achinyamata ambiri amasirira komanso kuwonetsa chidwi chofuna kupikisana nawo pa udindo wa Ndale ndicholinga chofuna kukapeza zinthu ngati Galimoto za pamwamba ati popeza iwowa amaona akuluakulu omwe ali pa maudindo akukhala ndi katundu wapamwamba ngakhale kuti akhala pa maudindo kwa nthawi yochepa.
Damison wati njira yabwino yodzichitira kauniuni mmoyo ndi kumvera lamulo loulula chuma chomwe munthu wapeza (assert declaration) uli mdindo m’boma. Iye waonjezera kuti nthambi za Boma monga Bungwe lothana ndi Katangale ndi Ziphuphu likuyenera kumadziwitsa anthu za ubwino woulula chuma chawo komanso kuzindikiritsa Mzika za dziko za ntchito za ma khonsolo, Bwanankubwa ndi komwe kungathandize kusamala chuma cha Boma.
Damison wathokoza atolankhani òmwe amadziwitsa a Malawi kaamba kolemba ndi kudziwitsa anthu za yemwe akuchita Katangale. “Atolankhani akugwira ntchito yotamandika kwambiri kuti tizidziwa kuti zinthu zimene zikuchitika ndi zotani”. Mkulu wa ku CISE Malawi-yu , wati ambiri a ndale akukhudzidwa ndi kupindula ku mchitidwe wa Katangale ndipo ndi atolankhani amene amatidziwitsa.
Malingana ndi Transparency Corruption Index, Dziko la Malawi liri pa nambala 115 pa maiko 180 omwe Katangale adamanga nthenje ndipo liri pa mlingo wa ma pointi makumi atatu ndi mphambu zinayi (34) pa mapointi zana limodzi(100)pothana ndi katangale ndi Ziphuphu.