Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

M’KUSOKA ZOVALA MULI PHINDU

Written by on October 22, 2024

Pa miringo ya zinthu zomwe zimalingidwa pali mulingo umodzi wokha umene umapereka mafunso   ngati kalingidwe kakusemba ndondomeko maka olingayo akakhala wa mamuna ndipo akulinga munthu wa mkazi. Chovala , ndi chithu chokhacho chomwe chimalingidwa ndi mmisiri wosoka.

Thomson Geza, Yemwe ndi mmodzi mwa wosoka zovala ku msika wa  Galliver mu mzinda wa Lilongwe, wavomereza kuti kusoka zovala ndi ntchito yovuta.”Tikhoza kunena kuti kusoka ndi kovuta chifukwa zimene udaphunzira ndi zina ,ndipo kawonekedwe ka zovala (design) kakumabwera tsiku ndi tsiku”.

Mkuluyu,wati   luso lake losoka ndi lakumtundu ndipo luntha lake lidatuphukira pamene amasoka kwa woyandikana naye nyumba. Mwayi utamugwera kuchokera ku TIVET,Thomson adapita kukachita maphunziro a za kasokedwe   ku Chiradzulu Vocation Training ,ndipo adapata Certificate ya ukadaulowu.

Waluso-yu, wanena kuti kusoka kuli ndi kuthekera kotukula dziko lino ngati aterela angakhale mmagulu. Ndikumagwirira ntchito limodzi yosoka zovala kaya za Chipatala,  Sukulu komanso zogwirira ntchito (worksuits). Iye, anatchulako zomwe zinkachitika mu nyengo ya muliri wa Corona Virus, kuti anthu amapatsidwa ntchito yosoka nsalu zotchingira pa Kamwa ndi Mphuno (mask) ndipo amazipanirira okha.

Mkuluyu wati amagwiritsa ntchito njira ya kasitomala oyambirira ndi yemwe athandizidwe koyambirira kupewa mgwazo.komabe  Thomson anachita changu kunena kuti angakhale kasitomala ochedwa kubwera amamusokera koma pa mtengo wina (express) osiyana ndi anzake kaamba koti amakhala waimitsa ntchito ya ena.

Malingana ndi Thomson, amasoka zomwe kasitomala wasankha osati Iyeyo.Mkuluyu, wanenetsa kuti ndi terala wolemera popeza kupyolera mu ntchito yakeyi wagula Galimoto,amakhala pa Nyumba yakeyake, kulipirira ana Sukulu, kugula Minda ndi zina zambiri.

Kumbali ya kubwera kwa Mtokoma wa makono,terala yu wati kwathandizira kwambiri kuphweketsa ntchito yawo.komabe, mkuluyu wati pali kusokoneza pang’ono kaamba ka kubwera kwa mtokoma wa makono.

Thomson, wapempha makasitomala ake kuti apitirize kusoketsa komanso wamema ena amene sadasoketsepo kwa katswiriyu kuti ayambe kusoketsa zovala kwa iye.

Thomson Geza ,amasoka zovala monga dilesi, zovala za fuko (national wears) komanso Malaya a abambo (shirts). Dziko la Malawi liri ndi  Sukulu zingapo zomwe zikuphunzitsa achinyamata kugwira ntchito za manja monga kusoka zovala.


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist