LITSIRO LA MKATI MWA THUPI
Written by Kradio on October 22, 2024
Litsiro ndi chinthu chokhacho chimene tsiku lake lobadwa silimadziwika ndipo limaberekana mwa kathithi. Mthupi mwa munthu namo mumakhala litsiro.
Namkungwi pa nkhani ya zakudya, Gladys Bandawe ,kuchokera ku Hope nutrition Services, watutumutsa mtundu wa a Malawi ponena kuti mthupi mwa munthu mumakhala litsiro.” Mkati mwathupi mumakhala litsiro limene limafunika kutsuka chimodzimodzi limene limakhala kunja kwa thupi”. Bandawe ,watsindika.
Namkungwi-yu wafotokoza kuti pali njira ziwiri zimene litsiro la mthupi limalowera. Iye,wati lina limachokera kunja kaamba kozunguliridwa ndi zinthu zosiyanasiyana ndipo litsiro lake limakhala ndi munthu aliyense ndi kukhudza tiziwalo ting’onoting’ono (cells) ,zimene zimabweretsa Matenda.Njira ina ndi litsiro lokudza mkatikati kaamba ka zakudya.
Bandawe ,watsimikiza kuti litsiro limachokera ku zotsalira za zakudya ngati urea yemwe amafuma ku zakudya zomanga thupi, zotsalira za chakudya cholimbitsa thupi ndi kuchokera ku zotsalira za mankhwala munthu akamachira. Iye, wati izi zimafunika kutuluka kunja kwa thupi.
Kumbali ya ziwalo zomwe zidapatsidwa kuthekera kochotsa zoipa mthupi,Gladys Bandawe,watchulapo Chiwindi(liver) ;chimene chimasefa mankhwala oopsa ku thupi(poisoni),Ipso (Kidney); zimene zimasefa nyasi mmagazi,Mapapo(lungs); amene amasefa nyasi kuchokera mu Mpweya(fumbi), Thumbo lalikulu(colon); limene limatulutsa nyasi za zotsalira za chakudya ndi Khungu(skin) ; limene limatulutsa nyasi kupyolera mu Chitungwi (thukuta), kuti ndi Ziwalo zimene pachirengedwe zidapangidwa kusefa litsiro la mthupi. Iye, wati ziwalozi zikalema zimapangitsa kuti mthupi mukhale litsiro. Bandawe, wachenjeza kuti ngati munthu amagwiritsa ntchito mankhwala onunkhiritsa khungu ( perfume) amene amakhukhutizidwa (roll on) ku Khwapa, ziri ndi kuthekera kotseka mabowo amene amathandizira kutulutsa zoipa kudzera mu thukuta.
Namkungwi-yu, watchula zinthu ngati kusowa kwa mitengo imene imabweretsa mpweya wabwino(oxygen), mankhwala opopera zakudya kuti zisungike kwa nthawi yaitali, mankhwala okolopera nyumba, mankhwala ochotsera fungo la kuchimbudzi, Sopo osambira, mankhwala obweretsa fungo labwino pa khungu(perfume), utsi otuluka ku Galimoto, mankhwala operekedwa ku ziweto, madzi akumwa amene aikidwa mankhwala okupha tizirombo, mankhwala ochizira thupi, mankhwala opopera mbewu, Matabwa amene akonzedwa ndi mankhwala ndi utoto(paint) owalitsira nyumba, kuti ndi zina mwa zinthu zimene zimakolezera litsiro mthupi.
Gladys Bandawe, watsindika kuti pali njira zochotsera (kusefa) nyasi mthupi monga Kumwa madzi ochuluka, kuchita masewero olimbitsa thupi, kusakhala ndi nkhawa ndi kudya zakudya zoonjezera (supplements) .
Malingana ndi kafukufuku wa Bungwe la Save the Children, dziko lamalawi liri pamwamba kwambiri mu maiko akumwera kwa Africa pankhani yosowekera zakudya zabwino kwa ana Malawi, iri ndi chiwerengero cha anthu pafupifupi 21 Million omwe akuyenda ndi litsiro mmatupi awo.