Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

MWINI NDALAMA

Written by on October 28, 2024

Pa zinthu zomwe munthu amaganizira tsiku ndi tsiku ndalama  imakhala pa mndandanda wa zinthu zoganiziridwa. Kaganizidwe kangwiro nako ndi kofunikira pa nkhani ya ndalama. Benard  ChiluzI, yemwe ndi Mkulu oyang’ana za maphunziro abwino a kayendetsedwe ka chuma ,wati kuganiza molungama ndi kaganizidwe komwe sikungamupezetse munthu mavuto kapena ndi kuganiza mu njira ina chifukwa cha zinthu zimene munthu akuwona, kumva ngakhale ku nunkhiza, kuganiza komwe kungamuthandizire kuti apite patsogolo.

A Chiluzi, atsindika kuti anthu sakusowa ndalama koma anthu alibe ndalama zokwanira zokuti agwiritse ntchito pokhala ndi zinthu zimene amafuna.”Vuto lalikulu padakalipano ndi lakuti anthu akusowa ndalama zokuti agwiritse ntchito pa zinthu zimene akufuna”.

A Chiluzi, apereka chitsanzo cha transformer kuti Boma limaika transformer mdera lanu chomwe ndi chitukuko chagulu, koma  zimatengera munthu kukoketsa magetsi  Nyumba mwake. “Chitukuko cha Maiko chimakhala cha gulu, zitengera munthu kukoketsa nthambo ya Magetsi, kuti akhale nawo Magetsi-wo”. Mkuluyu, watero pofuna kumveketsa kuti munthu payekha ayenera kuchitapo kanthu kuti apeze ndalama.

“Anthu a ndalama  samawayimbira likhweru.  Koma ukakhala opanda ndalama , umaitanidwa ndi likhweru”. Chiluzi ,watchula chizindikirochi.

Mkuluyu, watsutsa kuti ndalama si Satana.” Ikadakhala kuti Ndalama ndi Satana, bwenzi umphawi uli chiphasò chopitira kumwamba”. Mphunzitsi pa nkhani ya kayendetsedwe kabwino ka chuma-yu,watero.

Chiluzi,  wati anthu amene amaganiza bwino komanso ali ndi ndalama,  samadzidzimuka ndi zinthu ndipo waonjezera kuti ndalama zimadana ndi Phuma.” Tiyerekeze kuti ku Ofesi ,mumalandira uthenga wa pa lamya kuti ndalama  zalowa,  wina amatutumuka nkumakuwa kuti ‘zalowa!zalowa ‘ “.

Mkulu ophunzitsa  kayendetsedwe kabwino ka chuma-yu , wati anthu ambiri amaiwala kuti adzakalamba ndipo samazikonzekeretsa poikiza Ndalama  zokuti zidzawathandizire ku zaka za kumapeto a Moyo wawo, atatha kugwira ntchito.  Iye, wapempha anthu kuti asamalamuliridwe ndi ndalama  koma munthu adzilamulira ndalama.

Mkuluyu,  wati njira yabwino  imene munthu oganiza mwa ngwiro angapezere ndalama, ndi nthawi imene zinthu zavuta mdziko. Iye wapereka chitsanzo cha madobadoba, kuti amapanga ndalama  pamene mdziko  muli njala. Mkuluyu, wapitiriza kunena kuti anthu akachita ngozi, eni  kampani zokoka galimoto zomwe zachita ngozi amasangalala kuti apeza mopanga ndalama.  A Chiluzi  , anena izi pofuna kutsindika kuti munthu akuyenera kupeza njira  yothetsera mavuto  a mzake,  uku akupanga ndalama.

A Bernard Chiluzi, apempha anthu kuti adziikiza ndalama  uku akuzichulukitsa.”kubadwa osauka sikusankha koma kudzafa osauka ndi chisankho”. Iye, watsindika.

Malingana ndi bank yayikulu pa dziko lonse lapansi (World Bank), idapenekera kuti chuma cha dziko la Malawi, chikula ndi ma peresenti awiri okha ndipo umphawi upitirira kupita pa tsogolo.


Continue reading

Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist