CHUMA MU NYIMBO
Written by Kradio on November 13, 2024
Nyimbo ndi chinthu chokhacho chimene chimathuzitsa mtima pamene munthu ali m’chisoni, kukuza chimwemwe kwa munthu amene ali mchisangalalo komanso kuthandizira kugwira ntchito mosafooka.
Gulu la Peace Soldiers , lomwe limayimba chamba cha Reggae, lati lidabadwa mu chaka cha 2003 ndi cholinga chofuna kupeza njira pa kulankhula pa zomwe gululi linkadana nazo ku Sukulu ya Secondary.
Ngakhale gulu la anyamata anayi-ri lidayamba ndi uthenga odana ndi zinthu zina pa Sukulu ,lidakula nkuyamba kuimba mokhazikika kotero liri ndi zimbale zitatu zomwe zimatchedwa ‘Roots’ ndi Nyimbo zina.
Mmodzi mwa anthu mu gululi , wati kugwiritsa ntchito luso la Makono sikukubweretsa ndalama zokwanira.”Mbuyomu zinalibwino chifukwa munthu umadziwa kuti nditulutsa ma tepi okwana mwakuti ndipo ndalama zake zikhala mwakuti, koma pano ndi nkhani ya flash kapena WhatsApp, zikatero nyimbo zimakhala kuti zapita. Komabe ,kuyimba kwa pompopompo(live) kuli ndi kuthekera kobweretsa ndalama ,ndipo nyimbo zitha kukhala Geni”. Watero,mmodzi mwa anthu a gululi.
Akatswiri oyimba-wa, avomereza kuti oyimba ambiri mdziko muno alibe kuthekera kokhala ndi zida zoyimbira pompopompo. Komanso oyimba ambiri alibe akadaulo oyimba gitala.
Gulu la Peace Soldiers, lati cholinga chawo ndi kukhazikika poyimba pompopompo ndipo likugwira ntchito ndi a Waling Brothers komanso akukambirana ndi gulu la Disciples kuti agwire ntchito limodzi.
Gululi,lapempha akatswiri ojambula nyimbo mwa luso komanso mwa makono kuti abwere poyera ndi cholinga chakuti agwire ntchito limodzi ndi Gululi.”Sitikufuna munthu ojambula mwa kapwacha koma waluso”.mmodzi mwa anthu a gululi, wachenjeza.
Gulu loyimbali, lati masomphenya ake ndi kuyimba mokhazikika pompopompo nyimbo zosendezera anthu ku chifupi ndi Mlengi ndipo layamikira kuti chamba cha reggae, chimafunika kugwiritsa ntchito zida za pamanja, osati kudalira Kompyuta.
Akatswiri anayi-wa athokoza anthu amene amawatsata pomvera nyimbo zawo ndipo gululi lalonjeza kupitiriza kuyimba chamba cha reggae.
Gulu la Peace Soldiers , liri ndi ziwalo zinayi; Denis Kaira, Foster Blessing, Lusako Mkangama ndi Francis Banda. Zina mwa Nyimbo zomwe gululi layimba ndi “African Brown Sugar ndi “Mzinda woyera” kungotchulapo zochepa chabe.