MANYOWA NDI DILU
Written by Kradio on November 16, 2024
Zamoyo zirizonse zimayenera kulandira chakudya cha bwino kuti zidzikula ndi thanzi. Nayo mbewu ndi chimodzi mwa zinthu za Moyo zomwe zimafuna zakudya zabwino.A Tyson Chapuma, yemwe ndi Mlangizi pa nkhani za Ulimi ku Lunyangwa research station m’boma la Mzuzu , wati akugwira ntchito usiku ndi usana kufufuza za chakudya cha mbewu mu nthaka.
Pothirirapo mulomo pa nkhani ya kukwera mtengo wa Feteleza ndi kusakhazikika kwa ndondomeko ya Boma ya Affordable Input Program, Mlangizi wa za Ulimi-yu, wati anthu mdziko muno tikuyenera kuvomereza kuti manyowa ndiwo angatithandize.” Alimi tonse ku malawi kuno tingovomereza kuti tiyenera kugwira ntchito yopanga manyowa kuti tibwezeretse chonde mthaka. Ubwino wa manyowa ndi okuti ali ndi ntchito zambiri zimene amagwira mu nthaka kusiyana ndi kugwiritsa ntchito Feteleza ogula ku Sitolo, yemwe amakhala ndi nthawi yochepa mnthaka. Pamene tikathira manyowa, tizirombo tosintha mpweya kuti usanduke Michere timakhala kuti tiri pa Malo amene timawakonda , chinanso manyowa amasunga chinyontho”. Chapuma, wapereka ganizoli.
Mlangizi-yu wadandaula kuti alimi ambiri sakudzipereka popanga manyowa ngakhale adalandira uthenga wa kapangidwe ka manyowa. Chapuma, wapempha kuti tisinthe kaganizidwe kathu kuti tiyambe kuchita mwatsopano.
Mlangizi-yu, watchulapo mtundu wa manyowa wotchedwa Mbeya, yemwe ndi Manyowa amene amapangidwa posakaniza ndowa imodzi ya gaga, ndowa imodzi ya phulusa losefa, zitosi za nkhuku kapena ndowe za nkhumba zonyenyeka bwino, madzi a mlingo wa 5 litazi kapena mkodzo oyambirira okodzedwa mmawa wa mulingo omwewu.Zinthuzi zimamangidwa kwa masiku khumi ndi anayi kapena makumi awiri ndi mphambu imodzi mthumba lomwe mkati mwake mumakhala chipepara cha pulasitiki. Mkuluyu, wati Feteleza wa Chithumba ndi othandiza kwambiri.
Tyson, watsindika kuti dziko litha kupindula kwambiri pa Ulimi pogwiritsa ntchito manyowa a chithumba. Iye, walangiza alimi kuti adzitsatanso mlera nthaka, kubzala mitengo yothandizira kubwezeretsa chonde mthaka, kuchita a kalozera pambali pothira manyowa kuti nthaka isamalidwe.Mlangizi yu, wati njira ya kalozera imathandizira kubwezeretsa nthaka ndi kukolola madzi.
Chapuma, wati alimi asakaike pogwiritsa ntchito manyowa omwe ali ndi kuthekera kwakukulu kokolola chimodzimodzi mlingo wa mbewu omwe ungakololedwe pogwiritsa ntchito Feteleza. Mlangizi wa za Ulimi yu, wayamikira nthambi yoona za nyengo potulutsa ma lipoti a nyengo momwe ikumakhalira ndipo walangiza alangizi amnzake kuphunzitsa alimi za mbewu imene angabzale malingana ndi kusintha kwa nyengo.
Tyson, wapempha Boma kuti likhazikitse mfundo zokomera alimi kuti adzikhala ndi kuthekera kopeza manyowa.Ndipo wapempha adindo kuti agwire ntchito mwa mphanvu komanso wadzudzula mabungwe omwe siaboma amene akumangofuna kuyamikiridwa ndi anthu owathandiza osati kuti mlimi apeze phindu.
Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera, adalengeza ku dziko lonse lapansi kuti maboma 23 mwa Maboma 28 a dziko lino ali pa chiopsezo cha njala. Kafukufuku akusonyeza kuti anthu 4.2 Million dziko lino ali pa chiopsezo chosowa chakudya ndipo posachedwapa anthu ena m’boma la Machinga ,anafika pokudya chitedze kaamba kusowa Chakudya.