MUNTHU SUTHYOVA NJINGA ULI PA MTSETSE
Written by Kradio on November 16, 2024
Mutha kuvomerezana nane kuti mwasiya kaye zimene mumachita ndipo mukuwerenga nkhani iyiyi. Mukamaliza, muzikonzekeretsa kuchita zinthu zina. Izi ndi chimodzimodzi ndi kuzikonzekeretsa mmoyo omwe mungakhale mutapuma pa ntchito kapena bizinezi.
Benard Chiluzi, mphunzitsi wa kayendetsedwe kabwino ka chuma kuchokera ku old mutual, wadandaulira a Malawi kuti adzikhala akuikiza ndalama ngati njira imodzi yozikonzekeretsa kupuma pa ntchito. ” Chiri chonse chimene munthu umapanga umachipanga kwa kanthawi , imakwana nthawi yokuti zimenezija umasiya. Mphanvu zikakuthera ,udzidzatani?, udzikadyanji?, ukakhala moyo wa mtundu wanji?.Kulembedwa ntchito kapena kuchita Malonda sungapange uli ndi zaka makumi asanu ndi atatu. Tikuyenera kudzikonzekeretsa chifukwa mmoyo uno muli nthawi yopeza ndi nthawi yosapeza”. Chiluzi, watero.
Mkuluyu, wapereka chitsanzo cha kuthyova njinga, kuti munthu sumathyova njinga uli pa mtsetse. Umayenera kuzikonzekeretsa kuthyova njinga yo ukamakwera mtunda. Iye,wati munthu ukakhala pa bizinezi kapena ntchito, umakhala ngati uli pa mtsetse.
Chiluzi, wapempha anthu omwe ali pa ntchito yolembedwa kuti asamadalire ndalama za penshoni, popeza sizimakwanira kaamba koti imakhala theka la ndalama ngati zidzakhale zochulukirapo ndipo zotsalazo amazigawa pa zaka khumi. Iye,walimbikitsa anthu kuti adziikiza ndalama ku kampani ya Old Mutual , kuweta zifuyo ngakhale kumanga nyumba zobwereketsa. “Munthu okalamba wa pa ntchito kapena ochita malonda umasanduka bwenzi la Matenda.Ukakhala pa ntchito kapena Malonda, ukuyenera uzikonzekeretse kumadzalipirako ndalama za ku chipatala(medical scheme)”.
Mphunzitsi wakayendetsedwe kabwino ka chuma-yu , wati pali zifukwa zambiri zimene anthu akuyenera kuzikonzekeretsa poikiza ndalama ndi cholinga chokuti zidzawathandize iwo eni ngakhale okondedwa awo. Chimodzi mwa zifukwazi ndi ngozi ya maliro, yomwe imadza mwa dzidzidzi ndipo imapindula kwambiri kwa munthu amene amaikiza ndalama komanso imapeputsa anthu otsala pa ndalama zomwe akadagwiritsa ntchito poyendetsa mwambo wa Maliro.
Benard Chiluzi, wapempha anthu kuti akafika zaka makumi awiri ndi mphambu zisanu, akuyenera kudzikonsekeretsa ngati akupanga Malonda kapena walembedwa ntchito. Mkuluyu, wati ngakhale munthu atayamba kupeza ndalama ali ndi zaka makumi awiri, ndiwololedwa kuyamba kudzikonsekeretsa poikiza ndalama. “Kwa munthu amene ali ndi moyo ndipo akugwira ntchito, ali ngati munthu amene ali pa makina a mpweya wa okosijeni ndipo ikachotsedwa munthuyo amatha kufa”.
A Chiluzi, ati Kampani ya Old Mutual ndiyokonzeka kuphunzitsa anthu za kasungidwe ka ndalama mwa ulere.
Kampani ya Old Mutual, idayamba ntchito zake mchaka cha 1954 mdziko muno ndipo imalimbikitsa anthu kuikiza ndalama,kubwereka ndalama komanso ndondomeko zoyendetsera mwambo wa Maliro , pongotchulapo zochepa chabe.