ZOYENERA KUCHITA PA MALO OGWIRA NTCHITO
Written by Kradio on November 16, 2024
Malo ogwirira ntchito ali ngati nyambo mmanja mwa mnsodzi ndipo kugwira ntchito kumayika chimwemwe mtsaya pomwe malipiro akuperekedwa.Komatu kuzindikira ntchito yako nkofunika pa Kampani kapena bungwe limene munthu akuligwirira ntchito.
Mkulu ochokera ku Bungwe lolimbikitsa luso losiyanasiyana pakati pa achinyamata la CISE Malawi, a Davis Damison, wafotokoza kuti ndikofunikira kwambiri ngati bungwe kapena kampani kudziwa zolinga zawo ndipo anthu ogwira ntchito akuyenera kumadziwa zolinga za kampani kapena bungwe lawo.”Anthu akuyenera kudziwa zolinga za kampani kapena bungwe zazikulu ndi zazing’ono. Naye munthu ogwira ntchito akuyenera kukwaniritsa Masomphenya a kampani kapena bungwe komanso iye mwini ngati munthu”.
Damison , wati kudziwika pa ntchito ndi udindo wako nkofunika kwambiri kaamba koti kumathandizira kupereka chikhulupiliro kwa anthu ena komanso ogwira nawo ntchito pomwepo kuti kupereka maganizo,kuthokozedwa kudziyendanda bwino.Mkuluyu, wadzudzula anthu ena omwe amadzitcha okha ngati mabwana zomwe zimapereka chiphamaso komanso kukhalira ziganizo pa ntchito.
Pothirirapo ndemanga pa zomwe mabwana amayang’anira kwa ogwira ntchito ake,Damison wati mabwana mma kampani kapena mabungwe amayang’anira zimene ogwira ntchito analemba kuti akwaniritsa kumayambiriro kwa chaka.”Zolinga za mabwana zimadziwikiratu kumayambiriro kwa ntchito. Kwambiri mabwana amayang’anira masomphenya amene munthu wayika kuti akwaniritse pakutha pa miyezi khumi ndi iwiri”. Iye,wafotokoza.
A Damison, ati eni kampani ndi mabungwe akuyenera kupereka maphunziro a luso lopitirira( (continouus profession development)kwa anthu ogwira ntchito ake ndicholinga chofuna kupititsa patsogolo ntchito zake. Damison,wati izi zìmalimbikitsa kuti munthu akhale namandwa pothandizira mabungwe kapena kampani, kuti ntchito zake zipite patsogolo.
Mkulu wa Bungwe la CISE Malawi-yu, wayamikira ndondomeko ya uthenga wa makono( e-mail),kuimba lamya koma mobisa dzina la yemwe wapereka nkhawa zake komanso poika kabokosi kokuti anthu adziikamo nkhawa zawo pa momwe kampani kapena mabungwe akugwilira ntchito.
Davis Damison , wafotokoza kuti ma lipoti a momwe anthu ogwira ntchito amayenera kulemba pa momwe agwilira ntchito ndi ofunikira kwambiri kwa mabwana. “Malipoti ndi ofunikira kwambiri chifukwa zimathandizira kuwona momwe ntchito ikuyendera ,amathandiza kupanga ziganizo ndi kudziwa maluso ena omwe ogwira ntchito alinawo. Lipoti limadutsa pa zomwe munthu analemba kuti zikwaniritsidwa pa mwezi kapena pa chaka “.
Damison, wapempha anthu omwe akufuna ntchito kuti adziyesetsa kusunga zinthu ngati kalankhulidwe ndi kavalidwe ka momwe bungwe kapena kampani zimachitira.
Kafukufuku akusonyeza kuti dziko lino liri pa mlingo wa 67.86 percent wa anthu ogwira ntchito.