KADYEDWE KOYENERA PA UMOYO WA MUNTHU
Written by Kradio on February 26, 2025
Nzosakaikitsa kuti mphindi zingapo zapitazi mwangomaliza kumene kudya chakudya, ndipo mukatha kuwerenga nkhani-yi sizikhala zachilendo kuti Njala ikuimbirani likhweru kuti mudye chakudya chinachake.Koma nkhani yagona pa chakudya choyenera mthupi la munthu. Naomi Mvula, yemwe ndi katswiiri wotsatira kadyedwe ka bwino,watambasula za chakudya chabwino.
“Pali zakudya ma gulu asanu ndi limodzi .Zakudya zokhutitsa ; Chinangwa, Mbatata, Mawere, Mapira,Mpunga ndi Msima. Gulu lina ndi gulu la Nyemba ; Nandolo, Soya , Khobwe ndi Nyemba zimene. M’gulu la Masamba pali Nkhwani, Bonongwe, Kholowa, Therere ndi Masamba ena. M’gulu la Zipatso pali Mango, Nanazi ndi zipatso zina. Ndipo M’gulu la Mafuta ;pali Majalini , Mapeyala ndi Mtedza. Pamene m’gulu la Nyama ; pali Usipa, Ngumbi, Nyama imene. Tikamati zomanga thupi, ndi timichere tonse tochokera mmagulu asanu ndi limodzi “. a Mvula, atambasula.
A Mvula, atsindika za kufunika kwakudya zakudya za magulu anayi pa tsiku ngati zakudya zachepetsetsa. Iye, wapereka chitsanzo cha kudya chakudya ngati nsima ya masamba otendera komanso othiridwa Tomato.
Katswiri-yu, waulula kuti gwero la matenda a gasi komanso tizironda ta mmimba(Ulcers)ndi kudya zakudya za mbiri zomwe sizimagayika mokwanira ndipo zotsalira zake zimawola pamene chimbudzi chikupangika. Iye, watinso kupezeka kwa timiyala mchikhodzodzo , kukodza mkodzo wa Chikasu ndi gwero losamwa madzi ambiri.
Kwa anthu omwe amadya nsima mmamawa, katswiri-yu ,wati palibe vuto lirironse ngati munthu wakwanitsa kudya za magulu asanu ndi limodzi. A Mvula, ati madzi ndi ofunikiranso kwambiri chifukwa amathandiza kagayidwe ka chakudya mmimba.” Malingana ndi sayansi,65 percent ya munthu ndi madzi. Pamafunikira kumwa madzi a Mlingo wa Malita awiri; madzi amathandizira kuchapa ndi kusalaĺitsa thupi, kuthandizira kagayidwe ka chakudya komanso kuchotsa nyansi kupyolera mu thukuta”. Katswiri wa za kadyedwe kabwino-yu, wafotokoza.
Malingana ndi a Mvula, kuchita masewero olimbitsa thupi ndi abwino chifukwa thupi limakhala lochangamuka kotero mtima umaphunzira kupopa magazi bwino komanso amathandizira kuchepetsa Nthenda ya kuthamanga kwa magazi, pambali podwala matenda ena ngati Shuga, chimfine ndi zina. Iye ,wati kagonedwe nako kamakhala kabwino. Mvula wati anthu asamatutumuke ndi njala yomwe amamva pafupipafupi kaamba koti thupi likakhala kuti likuchita masewero olimbitsa thupi limafuna michere yambiri yopereka mphamvu.
Kumbali ya amayi oyembekezera, a Mvula ,alimbikitsa amayiwa kuti akuyenera kumadya moonjezerako pang’ono chifukwa samakhala akudya za iwo okha. Iwo , apereka chitsanzo chakuti ngati mayi amadya mitanda iwiri, akuyenera kuonjezerako theka la mtanda kuti thekhalo likagwire ntchito kwa mwana woyembekezeredwayo. Mvula , wachenjeza kuti amayi oterewa sibwino kuti adzidya moonjeza kwambiri kaamba koti thupi lawo litha kuyamba kudwala nthenda ya kuthamanga kwa mwazi.