Pa zinthu zomwe munthu amaganizira tsiku ndi tsiku ndalama imakhala pa mndandanda wa zinthu zoganiziridwa. Kaganizidwe kangwiro nako ndi kofunikira pa nkhani ya ndalama. Benard ChiluzI, yemwe ndi Mkulu oyang’ana za maphunziro abwino a kayendetsedwe ka chuma ,wati kuganiza molungama ndi kaganizidwe komwe sikungamupezetse munthu mavuto kapena ndi kuganiza mu njira ina chifukwa cha zinthu […]
Litsiro ndi chinthu chokhacho chimene tsiku lake lobadwa silimadziwika ndipo limaberekana mwa kathithi. Mthupi mwa munthu namo mumakhala litsiro. Namkungwi pa nkhani ya zakudya, Gladys Bandawe ,kuchokera ku Hope nutrition Services, watutumutsa mtundu wa a Malawi ponena kuti mthupi mwa munthu mumakhala litsiro.” Mkati mwathupi mumakhala litsiro limene limafunika kutsuka chimodzimodzi limene limakhala kunja kwa […]
Pa miringo ya zinthu zomwe zimalingidwa pali mulingo umodzi wokha umene umapereka mafunso ngati kalingidwe kakusemba ndondomeko maka olingayo akakhala wa mamuna ndipo akulinga munthu wa mkazi. Chovala , ndi chithu chokhacho chomwe chimalingidwa ndi mmisiri wosoka. Thomson Geza, Yemwe ndi mmodzi mwa wosoka zovala ku msika wa Galliver mu mzinda wa Lilongwe, wavomereza kuti […]
Kusowa kwa maphunziro a za Chuma pakati pa a Malawi kuli ngati kusowa kwa Chipatso cha Mpinjipinji Mnkhalango za dziko lino.Katswiri pa nkhani za Chuma a Innocent Banda, watsindika kuti ma Phunziro a za Chuma ndi osowa ngakhale ali ofunika. “Maphunziro a za chuma ndi ofunika chifukwa ndi chimene chimapereka mphamvu kwa anthu pothetsa umphawi,kutukula […]