ACHINYAMATA ADZUKA MU NDALE
Written by Kradio on August 21, 2024
Kwa nthawi yaitali Ndale za dziko la Malawi zakhala ziri ndi nkhope za anthu akuluakulu. Lerolino achinyamata adzuka kutenga nawo gawo mu Ndale.
Mkulu ochokera ku Generation 40,yemwenso amayankhulapo pa Nkhani zosiyanasiyana a Maloto Chimkombelo, avomereza kuti chiwerengero cha achinyamata omwe akuonetsa chidwi chofuna kusankhidwa mma udindo osiyanasiyana chachuluka.”Achinyamata ambiri akuonetsa chidwi chochita misonkhano yokopa anthu kuti adzawasankhe mmaudindo osiyanasiyana Chaka cha mawa(2025).Achinyamata ena apikisanapo pa Misonkhano yaikulu yosankha adindo mzipani. Zasiyana ndi kale pamene achinyamata amangotumidwa ndi a Ndale kuti adzidzipaka utoto ndi komanso kuti akakhape anthu”.
Ngakhale izi ziri chomwechi ,Katswiri-yu wati kusintha mkaganizidwe ndi limodzi mwa Mavuto omwe amabwezeretsa mbuyo achinyamata kutenga nawo mbali mu Ndale kaamba koti anthu akuluakulu ndiomwe anthu adawazolowera kuti ndiye ochita Ndale.Wachinyamata sikuti adzingolembetsa kuti akaponye voti ayi,akuyenera kupikisana nawo. Kusowa kwa Chuma chogwiritsa ntchito monga Kugulira mafuta a Galimoto komanso kugula msalu ndi zina zambiri zokopera anthu kuti adzawasankhe ndi Vuto linanso lomwe achinyamata akukumana nalo kuti apeze chikhulupiriro cha anthu kuti adzawasankhe.
“Kuchokera mu chaka cha 2013 kapena kubwerera mbuyo, achinyamata omwe ankachita za Ndale monga Malemu Lucius Banda,Billy Kaunda ndi Olemekezeka a Atupele Muluzi adabweretsa Kusintha. Mu 2014 a Atupele Muluzi , adabwera ndi Agenda for change( ung’onoung’ono).Mu 2014 yomweyo Mtsogoleri wakale wa dziko lino yemwenso adali mayi oyamba kukhaka mtsogoleri wa dziko kuno kwathu a Joyce Banda, adatengapo a Sosten Gwengwe ngati wachiwiri wawo mmene ankapita ku Masankho.Naye Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Muthalika adayenda ndi yemwe adali wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko lino Malemu Saulos Chilima pa Masankho a 2014. Achinyamata-wa abweretsa kusintha kwenikweni pa Ndale.Ndale zikumakhala zolimbikitsa mfundo kusiyana ndi kale pamene Ndale zimakhala zonyozana.Chifukwa cha kusefukira kwa achinyanata mu Ndale,abweretsa Ndale zosamba. Kukhala ndi akuluakulu okhaokha mu Ndale ziri ngati kuyendera phewa limodzi, achinyamata akuyenera kulolerana ndi kugwira ntchito limodzi ndi Mkhulang’ona pa Ndale”. Anafotokoza a Chimkombelo.
Katswiri-yu watsutsa kuti achinyamata asapatsidwe mpata kuti aphunzire Ndale.”Munthu sumaphunzira kuphika usali Kitchini.Achinyamata-wa akuyenera aphunzitsidwe Ndale ali mu Ndale momwemo”. Komabe a Chinkombelo adandauka ndi kusowa chidwi kwa achinyamata pa momwe Ndale zikuyendera pa dziko lonse lapansi.
Kumbali ya Zaka za munthu yemwe akufuna kuimira ngati Mtsogoleri wa dziko lino,katswiri-yu wapempha adindo kuti aunikirepo ndikutsitsa zaka kuti zikhale pakati pa 25 ndi 30. Malamulo a dziko lino amafotokoza kuti munthu oyimira utsogoleri wa dziko akhale ndi zaka zosachepera 35. Malingana ndi a Chimkombelo, mwa ovota 54 pa 100 aliwonse adali ndi zaka zapakati pa 18 ndi 35 mchaka cha 2019.
Mkulu wa ku Generation 40-yu walimbikitsa achinyamata kuti akhale olimba Mtima akafuna kuchita Ndale ponena kuti Ndale si za anthu a wedewede. Iye anapitiriza kupempha achinyamata kuti asachite mchitidwe onyoza kapena kukhapa anthu omwe ndiosiyana nawo zipani pamene Masankho a 2025 ayandikira.
Misonkhano yosankha adindo mzipani yomwe ikuchitika padakali pano mdziko muno yaonetsa kuti achinyamata akutenga nawo mbali pa Ndale. Mwachitsanzo, Chipani cha Malawi Congress, chiri ndi achinyamata Ngati a Richard Chimwendo Banda,a Madalitso Kazombo, kungotchulako ochepa chabe atatenga ma udindo akuluakulu mchipanichi.