ACHINYAMATA AZAVOTE PA MASANKHO MU 2025
Written by Kradio on August 18, 2024
Pamene zipani za Ndale zosiyanasiyana ziri kalikiriki kuchititsa misonkhano yosankha adindo(convention) omwe adzaimirire pa chisankho cha mchaka cha mawa, mmodzi mwa akuluakulu oyankhulapo pa nkhani za achinyamata mdziko muno a Davis Damison ,amema achinyamata kuti adzatenge nawo gawo pa Masankho a mchaka cha 2025 kuti akwaniritse kufikira zinthu zomwe amazifuna pokhala ndi adindo akumtima kwawo.
Nkuluyu wati, achinyamata ali ndi kuthekera kosintha zinthu mdziko muno potengera kuti chiwerengero cha anthu chomwe dzilo la Malawi lirinacho chochuluka ndi cha achinyamata omwenso akuvutika kwambiri.
“Tikatengera chiwerengero cha Bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la MEC cha mchaka cha 2022, chidaonetsa kuti achinyamata ndi ochuluka zedi ndipo akudutsa mu nyengo zovuta kwambiri. Akuluakulu ndi adindo ena atha kumadandaula kuti zinthu sizikuyenda koma atha kukhala kuti Malo adagula kale,buku la ku bank, ziphaso zoyendera(passport),ndi zina zambiri zomwe achinyamata alibe “.
A Damison ,afotokoza kuti achinyamata akasankha kusatenga nawo mbali posankha atsogoleri zimakhudza dziko mmagawo osiyanasiyana ngati umwini wa atsogoleri umasowa komanso ziganizo za adindo zabwino kaya zoyipa zimakhala zosakomera achinyamata. Ufulu owunikira adindo ngati sanakwaniritse kuchita malonjezano umasowa. Iwo anapitiriza kulimbikitsa achinyamata kuti kutenga nawo gawo posankha adindo kumathandiza kusintha ndondomeko zosinthira kayendetsedwe ka chuma cha dziko,Maphunziro,Ulimi ndi magawo ena.
“Wachinyamata atenge nawo gawo ku mbali yosankha adindo komanso kuimira ma udindo monga wa Mtsogoleri wa dziko,Phungu wa Nyumba ya Malamulo ndi Khansala”.
Damison wadzudzula mchitidwe wa andale ena omwe amakopa achinyamata powapatsa Ndalana kuti awasankhe koma akaenga udindo,samaonekanso. Iye wapempha kuti kukopa anthu kudzikhala kotsamira pa mfundo osati Ndalama.
Poyankhapo pa momwe gulu la achinyamata likuchitira mmaiko ena monga Kenya, nkulu yu wati ngakhale ziri zoopsa zomwe zikuchitika ndi maiko ena pomwe achinyamata akuchita zionetsero posagwirizana ndi mfundo za adindo, kuno kwathu atsogoleri amatha kuitana achinyamata ku Nyumba ya chifumu kuti akakambirane nawo pa mavuto omwe akuapsinja.
“Achinyamata amakhala ogwirizana malingana ndi mavuto omwe akukumana nawo. Mwachitsanzo ,dziko lino achinyamata ambiri akusowa ntchito , izi zimapangitsa kuti achinyamata abwere pamodzi”.
Nkuluyu wafotokoza kuti dziko lino liri ndi zotsamwitsa mmalamulo oyendetsera maboma ang’ono omwe samalola achinyamata kutenga nawo gawo popanga ziganizo zokhudza dziko ndipo izi nzofunika kuunikiridwa.
Davis Damison, wapempha makolo kuti awapange achinyamata kukhala mzika zodalirika powaphunzitsa makhalidwe abwino ndicholinga chokuti adzikhulupiridwa ndi anthu akamaimira maudindo osiyanasiyana.
Mzaka za 2019 ndi 2020, dziko lamalawi lidaona achinyamata ambiri atatuluka nkutenga nawo mbali yosankha Mtsogoleri wa dziko ndipo achinyamata ena adapikisana nawo m’maudindo ena.
Dziko lino likhala ndi zisankho za patatu (Mtsogoleri wa dziko,aPhungu a Nyumba ya Malamulo ndi ma Khansala) pa 16 September,2025.