BOMA LAPULUMUTSA BANK YAIKULU YA RESERVE
Written by Kradio on July 10, 2024
Boma la Malawi kudzera ku nthambi ya zachuma laonjola bank ya reserve ya mdziko mumo poipatsa ndalama zokwana 600 billion Malawi Kwacha kutsatira kuduka kwa bank yi ndi ndalama zokwana 539 billion Malawi.
Katswiri pa nkhani zachuma a Greenson Nyirenda ,ati dziko lino siridafike pokhazikika pa chuma. Kuduka pa chuma kwa bank ya reserve kukutanthauza kuti bank yi imagwiritsa ntchito ndalama zopyola kapezedwe kawo. Iwo anatchulako kusowa kwa Ndalama za kunja kwa dziko lino (forex)ngati chifukwa chimodzi chomwe chachititsa kuti bank yi itaye ndalama za nkhaninkhani chotere.
A Nyirenda apempha bank yi kuti iunikire momwe amapezera ndalama ndi momwe amagwiritsira ntchito ndalama kuti mavuto ngati awa asamakhalepo.Iwo ati Boma liike ndondomeko zothandizira kuti dziko lino likhale likupanga katundu omwe angamagulitsidwe kunja kwa dziko lino.
Pothirirapo ndemanga pa nkhani ya Ulimi,zokopa alendo ndi za migodi(ATM),katswiri yu anati ndondomeko yatsopanoyi ndiyogwira koma pakufunika kukhala ndi ndondomeko yabwino kumbali ya zosainira za migodi, ku ulimi tikuyenera kuusintha ulimi wathu kukhala geni. Kumbali ya zokopa alendo tikuyenera kukonza zinthu zina,misewu mwa chitsanzo msewu wa Nkhotakota. Kwakukulu tikuyenera tichite machawi kuti ndondomekoyi itipindulire.
Kumbali za migodi ,tikhale osamalitsa pokhala ndi akadaulo achimalawi (taonako akadaulo aku Sukulu za ukachenjede ngati MUST ndi MUBAS) omwe ali ndi kuthekera kusiyana ndi kumadalira akadaulo akunja omwe amadzangotibera ngati zija zidachitika ku mgodi wa
Kayerekera ku Karonga.Bungwe la Malawi Beaural of Standards likuyenera libwerepo pa nkhani ya kayezedwe ka miyala ya mtengo wapatali. Ku ulimi tikuyenera kulimbikitsa ulimi wa mthirira.
Greenson Nyirenda ,wati vuto la kugwa kwa ndalama ya kwacha itha kukhala mbiri yakale ngati dziko lino litalimbikitsa nkhani ya mafakitale kuti tidzitha kupanga zinthu zomwe zikagulitsidwa mmaiko ena zizitibweretsere ndalama za kunja kwa dziko lino.
Dziko la Malawi liri ndi ngongole zokwana 15.1 trillion Kwacha ndipo kugwa katatu kwa ndalama ya Kwacha kuyambira mchaka cha 2023 kufikira chaka cha 2024, kwachititsa kuti zinthu zambiri zikwere mdziko muno pafupifupi ndi 70% zomwe zakolezera umphawi.