BUNGWE LA ACB LIKUWODZERA
Written by Kradio on October 13, 2024
Ndizosabisa kunena kuti Moto wa khala la Mtengo wa Tsanya omwe umayaka ku Bungwe lothana ndi Katangale ndi Ziphuphu tsopano uli ngati Moto wa Mapesi.
Katswiri woyankhulapo pa nkhani za Utsogoleri wabwino komanso momwe zinthu zikuyendera mdziko muno Victor Chipofya, wati sakumva nkhani mma Nyuzipepala ngati momwe zinaliri mbuyomu .”Sitikumva zinthu mma Nyuzipepala ngati mmene timamvera mmene kunaliri Martha Chizuma, ngati kuchoka kwa a Martha Chizuma kwapangitsa kuti Bungwe lothana ndi Katangale ndi Ziphuphu la Anti Corruption Bureau (ACB ),lisamagwire ntchito yawo kapena likhale chete ndizokhumudwitsa kwambiri chifukwa Bungwe silimagwira ntchito ndi munthu mmodzi.A Chizuma anali wongotsogolera chabe komano kuli anthu ena okuti amakhala akugwira ntchito yawo tsiku ndi tsiku kuwonetsetsa kuti akuthana ndi Katangale ndi Ziphuphu”.
Chipofya, sanafune kubisa Mawu ndipo wati bvuto ndilakuti Bungwe la ACB, limatsogoza munthu.”Kwa nthawi yayitali timafuna kuti munthu mmodzi adziwonekera kwambiri kusiyana ndi Bungwe.Timatchula munthu mmalo motchula kuti Bungwe la ACB likufufuza kapena lamanga wakuti, chifukwa chake munthu akachoka kumakhala kuli chete”. Katswiriyu anaonjezera kunena kuti ntchito yomwe amagwira a ACB ndi ntchito yoopsya kotero amalimbana ndi anthu amene kwa iwo katangale ndi Mpunga wawo, ndi Chingwa chawo(chakudya chawo cha tsiku ndi tsiku). Iye walangiza kuti sipafunika kuulula dzina la munthu otsogolera ACB ,pamene akufufuza anthu koma kumanena kuti Bungwe ndicholinga chofuna kupewa adani.
Katswiri oyankhulapo pa nkhani za Utsogoleri wabwino-yu , wati ndizodetsa nkhawa kwambiri kuti kufikira lero Bungwe lothana ndi Katangale ndi Ziphuphu lidakalibe Mtsogoleri chichokereni a Martha Chizuma. Izi ati zikusonyeza kuti palibe chidwi kwenikweni chofuna kuthana ndi Katangale ndi Ziphuphu. Iye, wapempha Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera, kuti pachitike machawi kupeza Mtsogoleri wa Bungweli.
Victor Chipofya , wati pali chiopsyezo chokuti anthu atha kuyamba kunyinyirika kupereka misonkho ngati mabungwe ena a Boma akuchita zinthu zawo mobisa ponena kuti mabungwe wa amayendetsedwa ndi Misonkho ya a Malawi.
Powaika pa mlingo kunkhani yolimbana ndi katangale , a Chipofya ati a Chakwera alibe chidwi.” A Pulezidenti akhumudwitsa mtundu wa a Malawi ku nkhani ya kumenyana ndi Katangale ndi Ziphuphu. Mmene amayankhulira a Pulezidenti asadalowe pa mpando ndi mmene akuchitika zikusonyezeratu kuti alibe chidwi cholimbana ndi Katangale. A Pulezidenti amaoneka kuti anali ndi chidwi chomenyana ndi katangale ndi Ziphuphu ali Mtsogoleri wotsutsa Boma”. Chipofya,watero. Mtsogoleri wa dziko lino yu adalonjeza kudzachepetsa Mphanvu zake pa nkhani ya kasankhidwe ka mkulu wa Bungwe la ACB zomwe lero lino ndi Maloto a Chiwumba.
Chipofya , watchulapo nkhani ya Ndalama zomwe zinaperekedwa ku Bakery kuti zikagulidwire feteleza,Ndalama zina zogulira zipangizo za Ulimi zotsika mtengo zinaperekedwa ku Kampani yopanga Nsalu, komanso ku Bungwe logula Mafuta a Galimoto mdziko muno la NOCMA kudzera kwa Mlembi wa Mkulu mu ofesi ya Mtsogoleri wa dziko lino akupanga ziganizo zosemphana ndi mmene zikuyenera kukhalira. Iye, wati palibe chimene chachitikapo kufuna kuthana ndi izi.
Katswiriyu wati ngati pali Boma limene lidalowa ndi mafuno a bwino kuchokera ku mtundu wa a Malawi ndi Boma la Mgwirizano wa Tonse, koma mwayi wa chikhulupiliro cha Boma-li watayika ndipo Boma la Mgwirizano wa Tonse lataya lokha mwayiwu.
Victor Chipofya wati Katangale ali ngati Nthata ndipo Njira yabwino yolimbana ndi katangale ndi Ziphuphu ndikuphunzitsa ana za kuyipa kwa mchitidwewu adakali ku Sukulu za Pulayimale. Chipofya waperekanso ganizo lokuti munthu amene wapezeka akuchita Katangale akuyenera kumangidwa,kuzengedwa mlandu ndiponso adzilembedwa mu Nyuzipepala.
Mayi Martha Chizuma ,adasankhidwa pa 29 April 2021 kukhala mkulu wa Bungwe lothana ndi katangale ndi Ziphuphu kufikira pa 31 May 2024. Mkatikati mogwira ntchito yawo, a Chizuma adamangidwa ndi a Police m’mwezi wa September mchaka cha 2023.