Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

CENTENARY BANK YABEBA PA NKHANI YOGULITSA INSHULANSI

Written by on July 31, 2024

Pamene ngozi zagwa mwadzidzidzi anthu amakhala kakasi kusowa mtengo ogwira, izi ndi kutsatira kusakhala ndi ishulansi pa moyo wamunthu kapena katundu. Imodzi mwa bank yochita zinthu zake mwa makono ya Centenary, ili kalikiliki gugulitsa insurance kuti anthu asamatuluke thukuta zovuta zikaagwera.

Mkulu oyanganira ntchito za Bank-assurance ku Centenary bank a James Akuseka Msiska , wati Bank assurance ndi kubwera pamodzi kwa bank ndi insurance, “Timagulitsa insurance zosiyanasiyana mmalo mwa eni Kampani zomwe zimagulitsa insurance .Tiri ndi insurance ya Moyo(life insurance product), ndi insurance zina (general insurance) zokhudza Nyumba ndi katundu wina. Kuti munthu apeze insurance zi amayenera kutsegula akaunti ndi Bank yathu.”

A Msiska ati ku Centenary bank kuli phindu la mnanu munthu akatsegula akaunti ndikugula insurance kwa iwo.Mwa zina a Msiska ati Mitengo yogulira insurance ndiyomverera komanso Bank yi imathandizira kuunikira pa ngozi zomwe zachitika kutI anthu alandire Chipukuta misonzi kuchokera ku Kampani za insurance. Poonjezera apo a Msiska anati kwa omwe akufuna kudziwa za insurance kupyolera ku Bank ya Centenary, iwo amapereka uphungu mwa ulere.

“Mu nthambi zonse za Centenary bank mdziko muno tiri ndi insurance yokhudza Maliro (funeral cover) , yomwe imapereka danga poikapo akazi kapena amuna ako(ngati ndiwe okwatira/kukwatiwa),ana ako anayi osapyola zaka khumi ndi zisanu kudza mphambu zitatu(18) komanso Makolo ambali zonse. Pa malamulo adziko lino galimoto imayenera kuchitidwa insure,ife tiri nayo.kuphatikiza apo tiri ndi insurance yokhudza Nyumba, ya umoyo ( Cent-health insurance) , yomwe siikusankha olo munthu utakhala kuti uli kale ndi insurance ina. Insurance ya umoyo imagulidwa pa mtengo oyambira Mazana asanu ndi atatu ( 800 kwacha) kufika ma kwacha zikwi makumi awiri (20,000).

Tirinso ndi insurance ya Lamya za mmanja za makono, yomwe imathandiza pomwe munthu waberedwa kapena wagwetsa lamya ndipo yaonongeka. Insurance ya Nyumba zokhalamo kapena kuchitira malonda. Ndipo insurance ya zinthu ngati Nyumba ndiyotsikitsitsa poyerekeza ndi insurance ya galimoto.

Kwa omwe ali ndi lamya za makono atha kulembetsa pa Lamya pawo kuti apeze insurance yomwe akuifuna. Anafotokoza motero a James Msiska.

Nkulu-yu wapempha amalawi kuti akhale pa insurance popeza chakudza sichiimba ngoma.

Kafukufuku akuonetsa kuti chiwerengero cha anthu omwe ali pa insurance mdziko muno ndi pafupifupi 63%.

Bank ya Centenary idayamba kugwira ntchito zake mdziko muno kuyambira mchaka cha 2022 , ndipo iri ndi nthambi khumi,sizanu ndi mphambu imodzi(16).


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist