CHAKWERA WALAVULA MAKALA A MOTO KU UNGA
Written by Kradio on October 3, 2024
Mkuluwiko wokuti zingalume phula n’tenga ndi nkuluwiko omwe wamangirira uthenga omwe Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazalus Chakwera, anali nawo kwa mamulumuzana a Bungwe la mgwirizano wa Maiko apa dziko lonse lapansi.
Mmodzi mwa akatswiri omwe amayankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana mdziko muno a Dr George Chaima , ayamikira Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kaamba koyankhula ngati Mtsogoleri wa mu Africa. ” Apulezidenti atipula kwabasi ku United Nations General Assembly (UNGA)ndipo ayankhula ngati Mtsogoleri wa anthu osauka amu Africa. Mtsogoleri-yu sadapsatire mawu ponena kuti Bungwe la mgwirizano wa maiko onse la United Nations(UN),likupanga tsankho ndi Maiko ena osauka monga India ,Malawi ndi Democratic Republic Of Congo(DRC). Bungwe la UN, likumawasala mayiko wa. A Chakwera alamula kuti liwu la Africa pankhani za Chitetezo cha mu Africa lidzikhalapo ndipo lidzilankhulidwa ndi kuvomerezedwa ndi anthu oliyimira kumeneko ,osati kungonena kuti Africa ikaimiriridwe ndi anthu awiri koma asakayankhule kanthu, komwe kuli ngati kukana Africa kuti ndiyopanda nzeru , iribe mawu a Mphamvu”. Watero katswiri-yu.
Malingana ndi Dr Chaima ,ati Dr Chakwera akhudza mbali yoyenera ku mkumano-wu zomwe dziko lino limafuna kudziwa. “Sibwino Mtsogoleri kupita ku Msonkhano ngati uwu ndikumakangoyamikira Maiko a anthu olemera pamene ndi iwowo akutipangitsa ife anthu a mu africa kukhala amphemvu mdyera kumthiko (osaukitsitsa). Ndibwino kumawauza zoona Angerezi, chifukwa ndi iwo adatipangitsa ife kukhala atsamunda, ndipo adali ndi zolinga zabwino kwa iwowo osati ife. Ife ngati ma filika tikudziwa kuti Mgerezi adatikola kuti tikhale atsamunda ndi cholinga chofuna kutipondereza ”. wafofokoza motero Dr George Chaima.
Kumbali ya Ngongole zomwe Maiko a mu Africa akulephera kuwonjoka nazo ku Maiko olemera , Mtsogoleri wa dziko lino wapempha Maikowa kuti akhululuke Ngongole-zi. Ndipo Dr Chaima wayamikira izi.” Afrika wadzadza ndi ngongole, tiyang’ane ku Malawi kwathu kuno tiri ndi Ngongole yambiri. Mukati muyionetsetse ngongoleyi tikukanika kuyibweza ,mmalo mwake tikupitirapitira kukatenga Ngongole ina zomwe ndi kukonza ndondomeko yokankhira a Malawi ku Umphawi. Kuyankhula kokuti ngongole muthetse ndi kuyankhula kwa chining’a zomwe zikutanthauza kuti maiko wa atibwezere zathu zomwe adatenga. Angerezi akamatipatsa ngongole amakhala akubweza zathu zomwe amatenga kwathu kuno monga Miyala ya mtengo wa patali”. Watero Chaima.
Dr Chaima, wati sichanzeru kuti Maiko a mu Africa adzibwereka Ndalama.” Mchitidwe wa Ngongole ukuyenera kutha. Mwachitsanzo, kuno ku Malawi tiri ndi Bungwe lotorera Misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA), ndi magawo ena ,koma vuto Ndalama zomwezo timabweza Ngongole kwa Angerezi,kugula Mankhwala mzipatala, kuchitira zitukuko komanso Ndalama yomweyo imabedwa kudzera mu Katangale ndi atsogoleri”. Pothirirapo ndemanga pa ndondomeko yopereka Ngongole kwa kanthawi (Extended Credit Facility) katswiri-yu, wati mabungwe a International Monetory Fund (IMF) ndi World Bank, ndi ‘zigawenga’ zomwe zimachita dambisi (kudana) ndi Maiko a mu Africa.” Mabungwewa amakamba nkhani za Ngongole nthawi zonse ndicholinga chokuti apindule iwowo.Ngati sakupeza Ndalama mokwanira, amaika ndondomeko zokuti tichepetse Mphamvu ya Ndalama yathu zomwe zimapangitsa kukwera kwa mitengo ya katundu pa Msika. Tikuyenera tisiye kumadalira ma Bungwe wa”. Iye watero.
A Chaima ,adandaula kuti dziko lino liri ndi Nyanja zisanu, miyala ya mtengo wapatali koma sitimazigwiritsa ntchito.
Katswiri yu wapempha utsogoleri womwe ulipo padakali pano ndi aMalawi onse kuti asinthe kaganizidwe ndikuyamba kugwiritsa ntchito zinthu zomwe dziko lino liri nazo pofuna kutumphula Chuma cha dziko lino.
Dziko la Malawi liri ndi chiwerengero cha anthu opyola 21 Million . Malingana ndi unduna wa za Chuma, dziko lino liri ndi Ngongole yokwana 15.1 trillion kwacha.