CHIKHALIDWE CHA AMALAWI CHASULUKA
Written by Kradio on August 4, 2024
Zakudya, mavalidwe ,Nyimbo ndi Miyambo ndi zina mwa mbendera zomwe zimaulula za Chikhalidwe cha munthu. Makono dziko lapansi likuyenda ngati mudzi umodzi kaamba ka chitukuko chogwiritsa ntchito makina monga Lamya ndi ma Kompiyuta.
Mfumu yaikulu Lukwa ya M’boma la Kasungu yadandaula kuti a Malawi ataya Chinkhalidwe chawo potengeka ndi zochitika zomwe amawona Mmaiko ena.”Dziko la pansi liri pa mbalambanda kotero kuti palibe chobisika.Mwana akangokwanitsa zaka zisanu ndi zinayi(9), amakhala akudziwa chirichonse chomwe chikuchitika pa dziko li”.
Gogo chalo-yi yapempha Mafumu, adindo a Mpingo ndi Makolo kuti ayesetse kuphunzitsa achinyamata za chikhalidwe chawo cha chi Malawi.”Sikuti anawa tisawapatse makina amakono ngati Lamya za pamwamba,ma Kompiyuta ndi zina kuti adzigwiritsa ntchito. Izi ndizothandiza ndithu malingana ndi momwe dziko likuyendera koma tiyambe tawaphunzitsa anawa za chikhalidwe chathu”.
Pofotokoza za kusasunga chikhalidwe chathu,Mfumu yaikulu Lukwa yati achinyamata amaona kuti m’badwo wawo ndi woyenda mwa makono ndipo akuluakulu(makolo) ndi m’badwo otsalira pogwiritsa ntchito makina a makono.
Mfumuyi yadzudzula Makolo omwe amangosiira udindo aphunzitsi kuti ndiwo aphunzitse achinyamata za Chikhalidwe chawo.”Makolo ambiri akuchita ulesi pophunzitsa ana za Chikhalidwe chathu. Panopa Makolo akumakangosiya ana awo pa galimoto ku Sukulu,nkukawatenga kusiyira udindo onse aphunzitsi kuti ndiwo aphunzitse Chikhalidwe”.
“Pali chiopsezo kuti m’badwo wathu ukatha,achinyamata-wa ngati sitiwaphunzitsa za Chikhalidwe chathu kudzakhala Malawi wa chilendo” . Yachenjeza Mfumu-yi. Gogo chalo-yi yaonjezera kunena kuti a Malawi ambiri safuna kunena zabwino za dziko lawo.
Mfumu yaikulu Lukwa yadzudzula ndi’nso kupempha a Malawi ena kuti asiye mchitidwe wosalimbikira ntchito pomangodalira kuthandizidwa ndi Boma.”Dzikoli siringatukuke ngati tidzidalira ena kuti ndiwo atithandize.Pakhomo pa munthu pamafunika pakhale pa mwana alirenji osati kungolima kamodzi kokha pa Chaka kwinaku nkumangoyenda Bawo.Mayiko a anzathu adatukuka chifukwa amagwira ntchito kwa Chaka chonse, usana ndi usiku “.
Dziko la Malawi lidayamba kutaya chikhalidwe kwambiri utangotha ulamuliro wa Chipani chimodzi chomwe ankatsogolera ndi Mtsogoleri oyamba wa dziko lino Malemu Dokota Hastings Kamuzu Banda.