Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

DZIKO LA MALAWI LITAYA ACHINYAMATA

Written by on August 4, 2024

Mukayenda mmakwalala,nzikhuthe ,malo ochitira ma sewero osiyanasiyana ndi kwina komwe achinyamata amasonkhana mupeza kuti pakati pawo pamakhala chikoka cha kugawana zakumwa ndi Fodya . Zambiri mwa izo  zimakhala Mankhwala ozunguza ubongo.

Katswiri pa thanzi la kaganizidwe ka ngwiro a Joseph Maseke, ati Mankhwala ozunguza ubongo ndi Mankhwala omwe mkati mwake muli zinthu zosokoneza ubongo.

“Pali zambiri zimene zimayambitsa kuti achinyamata ayambe kugwiritsa ntchito  Mankhwala ozunguza ubongo. Makamaka kuno ku Malawi pali zifukwa ngati kunamizana pakati pa achinyamata, kusowa zochita,  kukhala dera lomwe zochitika zake ndi zosokonekera ,kukhala kwambiri ndi nkhawa komanso kubadwa ndi makhalidwe ovuta”. Anafotokoza a Maseke.

Pa zotsatira za kugwiritsa ntchito Mankhwala ozunguza ubongo, Katswiri-yu wati ngati kumbali yamaphunziro , munthu samachita bwino . Kuchoka kwa thanzi la mkaganizidwe ka ngwiro, Kucheza zosiyana ndi amzako ,umbava komanso kupalamula Milandu yosiyanasiyana.

Joseph Maseke, wadzudzula makolo omwe amatuma ana kukagula mankhwala oopsa a Cocaine komanso mchitidwe omwe achinyamata ena akumachita pomagula mankhwala monga achifuwa amadzimadzi ndi mankhwala ena nkumasakaniza ndi zinthu zina zomwe ndi zosemphana ndi cholinga cha omwe adapanga mankhwala -wa.

“Pali chiopsezo choti tidzasowa achinyamata oti agwire ntchito zosiyanasiyana tikalekerera mchitidwe oyipawu.Mwachitsanzo, Mmalo okwerera Basi, muona muli achinyamata omwe nkhope zawo siziri bwino zomwe zikusonyeza kuti akumagwiritsa ntchito Mankhwala ozunguza ubongo “. Iwo anafotokoza.

Katswiri-yu wadandauka kaamba ka kuchepa kwa Ndalama zopita ku unduna wa za umoyo kuti zikathandizire nthambi ya kaganizidwe ka ngwiro. Iye, anachita changu kuyamikira zipatala zomwe si za Boma ndi Mabungwe oyima paokha kaamba koyesetsa kuphunzitsa achinyamata za kuipa kogwiritsa ntchito Mankhwala wa .


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist