Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

KADYEDWE KOYENERA PA UMOYO WA MUNTHU

Written by on February 26, 2025

Nzosakaikitsa kuti mphindi zingapo zapitazi mwangomaliza kumene kudya chakudya, ndipo mukatha kuwerenga nkhani-yi sizikhala zachilendo kuti Njala ikuimbirani likhweru kuti mudye chakudya chinachake.Koma nkhani yagona pa chakudya choyenera mthupi la munthu.  Naomi Mvula, yemwe ndi katswiiri wotsatira kadyedwe ka bwino,watambasula za chakudya chabwino.

“Pali  zakudya ma gulu asanu ndi limodzi .Zakudya zokhutitsa ; Chinangwa, Mbatata, Mawere, Mapira,Mpunga  ndi  Msima. Gulu lina ndi gulu la Nyemba ; Nandolo, Soya , Khobwe ndi Nyemba zimene. M’gulu la Masamba pali Nkhwani, Bonongwe, Kholowa, Therere  ndi Masamba ena. M’gulu la Zipatso pali Mango, Nanazi ndi zipatso zina. Ndipo M’gulu la Mafuta ;pali Majalini , Mapeyala ndi Mtedza. Pamene m’gulu la Nyama  ; pali Usipa, Ngumbi, Nyama imene. Tikamati zomanga thupi, ndi timichere tonse tochokera mmagulu asanu ndi limodzi “. a Mvula, atambasula.

A Mvula, atsindika za kufunika kwakudya zakudya za magulu anayi pa tsiku ngati zakudya zachepetsetsa. Iye, wapereka chitsanzo cha kudya chakudya ngati nsima ya masamba otendera komanso othiridwa Tomato.

Katswiri-yu, waulula  kuti gwero la matenda a gasi komanso  tizironda ta mmimba(Ulcers)ndi kudya zakudya za mbiri zomwe sizimagayika mokwanira ndipo zotsalira zake zimawola pamene chimbudzi chikupangika. Iye, watinso kupezeka kwa timiyala mchikhodzodzo , kukodza mkodzo wa Chikasu ndi gwero  losamwa madzi ambiri.

Kwa anthu omwe amadya nsima mmamawa, katswiri-yu ,wati palibe vuto lirironse ngati  munthu wakwanitsa kudya za magulu asanu ndi limodzi. A Mvula, ati madzi  ndi ofunikiranso kwambiri  chifukwa amathandiza kagayidwe ka chakudya mmimba.” Malingana ndi sayansi,65 percent ya munthu ndi  madzi. Pamafunikira kumwa madzi a Mlingo wa Malita awiri; madzi amathandizira kuchapa ndi kusalaĺitsa thupi, kuthandizira kagayidwe ka chakudya  komanso kuchotsa nyansi  kupyolera mu thukuta”. Katswiri wa za kadyedwe kabwino-yu, wafotokoza.

Malingana  ndi a Mvula, kuchita masewero olimbitsa thupi ndi abwino chifukwa  thupi limakhala lochangamuka kotero mtima umaphunzira kupopa magazi bwino  komanso amathandizira kuchepetsa Nthenda ya kuthamanga kwa magazi, pambali podwala matenda ena ngati Shuga, chimfine ndi zina. Iye ,wati kagonedwe nako kamakhala kabwino. Mvula wati  anthu asamatutumuke ndi  njala  yomwe amamva pafupipafupi kaamba koti thupi likakhala kuti likuchita masewero olimbitsa thupi  limafuna  michere yambiri yopereka mphamvu.

Kumbali  ya amayi  oyembekezera, a Mvula ,alimbikitsa amayiwa kuti akuyenera kumadya moonjezerako pang’ono chifukwa  samakhala akudya za iwo okha. Iwo , apereka chitsanzo chakuti ngati  mayi amadya mitanda iwiri, akuyenera kuonjezerako theka la mtanda  kuti thekhalo likagwire ntchito kwa mwana woyembekezeredwayo. Mvula , wachenjeza kuti amayi oterewa sibwino kuti adzidya moonjeza kwambiri  kaamba koti thupi lawo litha kuyamba kudwala nthenda ya kuthamanga kwa mwazi.


Continue reading

Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist