Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

KATANGALE NDI ZIPHUPHU WAYALA MPHASA

Written by on August 21, 2024

Nzosabisa kuti makono munthu ukafuna kupeza chinthu mosavuta kuchokera kwa adindo umayenera upereke Ndalama ya ‘fanta’. Izi zikapanda kuchitika zimakhala ngati tsiku si tsikunso.

Dr. George Chaima, ati kubwera kwa ufulu okhala ndi zipani zambiri (demokalase) ,wakolezera mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu.”Kuyambira mchaka cha 1964 kufikira mchaka cha 1992,Malawi adali dziko lokoma. Munthu umatha kusiya galimoto panjira osaikhoma ,umaipeza bwinobwino penanso ikakufera panjira umatha kuthandizidwa popanda kufunsidwa kuti upereke kenakake. Demokalase ndi dzina lomwe litabwera , a Malawi sadalimvetsetse. Adamva kuti ndiko kuchita katangale ndi ziphuphu .

Andale, ogwira ntchito m’boma ndi ochita malonda akuluakulu(amwenye), ndi gulu la anthu omwe akuchita katangale ndi ziphuphu zomwe zikusaukitsa (kugwetsa) dziko lino.”

A chaima afotokoza kuti Kudzikonda,Kusakonda dziko ndi Ulesi, ndi zifukwa zomwe zikulimbikitsa katangale ndi ziphuphu. Iwo ati mwachitsanzo , ku Police ,munthu umafunsidwa kuti upereke Ndalama ndicholinga choti upatsidwe belo.Nako ku bungwe lowona zotuluka ndi kulowa mdziko muno ndi ku bungwe lopereka ziphaso zoyendetsera Galimoto,munthu umauzidwa kuti ukumane ndi dobadoba ukafuna kulandira thandizo mwa msanga.

Pothirirapo ndemanga pa zomwe Boma laTonse Alliance lidafotokozapo kuti mbava zenizeni ndizo zikuyenera kupita ku Ndende, okuba Nkhuku atulutsidwe ku Ndende ko ,Mkulu-yu anati izi zinali Nkhambakamwa chabe.”Ndindani wa Ndale yemwe adalakwa ali ku Ndende? Mesa amangosuzumirako nkumabwerako. Uzeni Nduna yomwe ili ku Ndende? Simupezako aliyense wa Chuma ku Ndende. Ku Ndende kumakhala anthu osauka kwambiri”.

Dr Chaima , wati Masomphenya a Malawi 2063 alingati pepala lomwe munthu utha kuliwotcha.Malawi vission 2020, yomwe idanyamula uthenga oti pofika mchaka cha 2020,munthu asamwalire ndi Matenda a Malungo komanso kupeza Madzi a ukhondo mwa zina, idalephera kukwaniritsidwa. Iwo apempha adindo kuti ayesetse kukwaniritsa Maloto a 2063 omwe ati ndi apamwamba.

A Chaima ,achenjeza adindo kuti asakomedwe ndi mchitidwe wa Katangale ndi ziphuphu ponena kuti ili ndi dziko limatembenuka.Mkuluyu wa pempha a Malawi kuti akonde dziko lawo ndipo agwiritse ntchito bwino Ufulu wawo posankha adindo omwe sakhudzidwa ndi nkhani za Katangale ndi ziphuphu mchaka cha mawa pomwe dziko lino likuyembekezera kukhala ndi Chisankho chachikulu.

Dziko la Malawi ndi losaukitsitsa kwambiri  pa dziko  lonse lapansi. Malingana ndi kafukufuku wa bungwe la Transparency corruption Index ,Malawi ali pa nambala 115 mwa Maiko 180 komwe kumachitika katangale kwambiri.

Nkhondo yolimbana ndi Katangale ndi ziphuphu yakhala ili yotsamwitsa mdziko muno. Chaka chatha yemwe adali mkulu wakale wa Bungwe lolimbana ndi kuthana ndi katangale ndi ziphuphu  a Martha Chizuma, adanjatidwa ndi a Police pamene  amafufuza Milandu ya katangale yokhudza anthu a Ndale ndi ochita Malonda akuluakulu.


Continue reading

Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist