KODI CHUMA CHA ZIPANI ZA NDALE CHIMA CHOKA KUTI?
Written by Kradio on December 27, 2024
Mawu akuti bongololo sadzolera mafuta pa gulu akugwirizana kwambiri ndi zomwe zipani za ndale zimachita pa nkhani youlula komwe kumachokera chuma chake.
Victor Chipofya, yemwe ndi katswiri pa nkhani za ndale wati aMalawi samamvetsetsa momwe ndalama zoyendetsera zipani zimachokera.”Nthawi zambiri Chipani chokuti chiri kotsutsa chikangolowa m’boma chimayamba kugula magalimoto ankhaninkhani.Izi zimadabwitsa kuti ndalama azitenga kuti?.Nchifukwa chake Mlembi wamkulu wa kalembetsedwe ka Zipani ,padakhazikitsidwa kuti padzikhala kuulula kwa komwe zipani zimatenga ndalama zawo chifukwa chakuti nkhani imeneyiyi ikulumikizana kwambiri ndi nkhani ya Katangale”.
Chipofya, wati akuganizira kuti kochokera chuma cha zipani za ndale zimalumikizana kwambiri ndi katangale ndi ziphuphu. Iye, wati nthawi zambiri anthu amene amapereka ndalama ku zipani zikakhala kumbali yotsutsa amafuna kuti adzapeze danga lapaderadera zipanizi zikadzalowa m’boma ngati ma contract ndi bizinezi zosiyanasiyana.
Chipofya,wati a Malawi ali ndi ufulu odziwa komwe ndalama zoyendetsera zipani zimachokera.” Zipani za ndale ndi mabungwe a amalawi.A Malawi ayenera kudziwa kuti ndalama zoyendetsera zipani zikuchokera kuti”. Katswiri-yu wati kusaulula komwe ndalama zoyendetsera zipani zimachokera ndi zoopsya chifukwa zikhoza kupititsa patsogolo mchitidwe wa Katangale ndi ziphuphu.
Chipofya wadandaula kuti anthu ambiri akuvutika ndipo zipani sizikulabada komanso anthu a ndale amazitenga ngati aliyense ochita ndale azikhala wa chuma zomwe sizabwino. Chipofya ,wati cholinga chenicheni chokhazikitsira chipani cha ndale sikuoanga bizinezi koma kuyendetsa dziko.
Pathandizo lomwe limachoka kwa anthu ena kulimbikitsa chipani.Chipofya wayamikira mchitidwewu komabe wadabwa kuti zipani zambiri sizimapanga chonchi.” Ndi chifukwa chiyani zipani zambiri zimadikira anthu ena awathandize ndi khobidi pamene ali ndi anthu owathandiza kuti zipite patsogolo?” . katswiri-yu wadabwa.
Victor Chipofya,wati ntchito yothetsa Katangale ndi ziphuphu ndi kukhala ndi umunthu ndi mtima ofuna kuthetsa mchitidwe wu. Iye, akugwirizana kwathunthu ndi ganizo lakuti zipani zidzisindikiza komwe ndalama zake zimachokera.
Pa kuchuluka kwa zipani za ndale mdziko muno, Chipofya sanavomere kapena kuti ndizolakwika kapena ayi. Iye, wati izi ndi zimene a Malawi adasankha mu 1993. Komabe, katswiri-yu wati zolinga za kakhazikitsidwe ka zipani sikakhala kuti kakudziwika bwinobwino.
Pa zaka 60 zomwe dziko lino lakhala liri pa ufulu odzilamulira,Chipofya wadandaula kuti zipani za ndale zimalonjeza zomwezomwezo koma sizimakwaniritsa kuchita malonjezano awo.”Zipani zambiri zimalonjeza zomwezomwezo; Feteleza, chakudya,Mijigo….”.