Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

KUCHOKA PA GENI YOYENDA NAYO NKUKHALA MWINI SHOP

Written by on July 10, 2024

Tsiku silitha pasadachitike malonda aliwonse. A Zebron Lewis ochokera ku area 9 mu mzinda wa Lilongwe akhala akuchita geni. Bambo Lewis adayamba ndi geni yogulitsa Nyemba poyendanazo ku area 24, zaka zingapo zapitazo. Kuchulukana kwa anthu ogulitsa malondawa ku area 24,kudawapangitsa a Lewis kumakachitirageniyi ku area 25 ndi 49. Pakupita kwa nthawi nkuluyu adasintha mtundu wa geni nayamba
kugulitsa Sopo. Iyeyu amagulitsa sopo poyendayenda naye ndipo ankagulitsa Surf ndi Omo. A Lewis atapeza phindu mu geniyi adaganiza zotsegula Kantini . Iwo adayamba ndi ma siwiti ndipo Kantiniyi idakula.

“Chimene chimafunikira kwambiri kuti ndikhale ndi anthu ondigula kwambiri ndiko kugulitsa zinthu zanga pa miringo ndi mitengo yofikirika “.Kupatula apo,ndimawasekerera ondigulawa komanso kuwathandiza moyenerera.Kantiniyi ndimaitsegula mma 5koloko mmawa kuchitira awo omwe amafuna kugula zinthu mofulumira asadapite ku ntchito, anafotokoza motero a Lewis. Kupyolera mu Kantini yaku area 49,

Bamboyu wakwanitsa kutsegula Kantini ina kwawo ku Ntcheu ndiponso ali ndi Malo owonetsera wailesi ya Kanema. Nkuluyu akufunitsitsa atatsegula Kantini yopikulitsa zinthu. Khama lipindula!


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist