KUKONZEKERA KUKHALA NDI NDALAMA ZOKHAZIKIKA
Written by Kradio on May 31, 2025
Pa chirichonse chimene munthu amachita kukonzekera kumafunikira. Zinthu zikamachitidwa zosakonzekera zimaonekera ng’amba. Ndalama nayo kuti ikhazikike imafunika kuyikonzekera.
Mphunzitsi wa maphunziro abwino a kayendetsedwe ka chuma kuchokera ku Old Mutual, Benard Chiluzi watsindika za kufunikira kokhala ndi Ndalama zokhazikika. “Pali anthu ena Ndalama sizimawavuta kupeza, pali anthu ena Ndalama zomwezi zimaathawa.Tikamakàmba za kukhala ndi Ndalama zokhazikika ndipamene munthu akukhala ndi Ndalama mnyengo zonse za moyo wake, kuphatikizaponso apabanja ake”. Iye, wafotokoza.
Chiluzi, wati zimakhala zomvetsa chisoni kuwona ana akuvutika chonsecho makolo awo anali a ndalama asadamwalire. A Chiluzi , adzudzula anthu omwe amangokhaliratu osachitako zinthu zobweretsa ndalama Mmoyo kapena kudalira njira imodzi yowabweretsera ndalama. Iye, wapereka chitsanzo cha ganizo la Mtsogoleri wa dziko la America,Donald Trump, yemwe atangolumbira kumene kukhala Mtsogoleri wadzikolo adayimitsa ntchito za mabungwe ambiri mmayiko a anthu osawuka ngati Malawi. Mkuyankhula kwake , Chiluzi wati anthu ambiri amene amangodalira ntchitoyi akuvutika kwambiri.
Mphunzitsi-yu walimbikitsa anthu kumachitako geni zosiyanasiyana ndi cholinga chofuna kukhala ndi Ndalama zokhazikika komanso kumagwiritsa ntchito Ndalama pa zinthu zofunikira mmoyo ngati chakudya ndi zina.
Kumbali ya zinthu zokugwa mwa dzidzidzi, Chiluzi wati munthu akuyenera kumalamulira ndalama zake osati ndalama imulamulire. Mkuluyu , wapemphanso anthu kuyikiza ndalama mu ndondomeko zomuthandizira nthawi ya Ngozi.Iye, watsindika za kukonzekera popereka chitsanzo cha Chitute , chomwe chimasakiratu chakudya chokudya mnyengo ya dzinja. Chiluzi,wati munthu ukamapalasa njinga pa mtsetse sizitanthawuza kuti kulibe Mtunda.
Mmodzi mwa anthu omwe apindula pokonzekera zinthu zokugwa mwa dzidzidzi mu dongosolo la ndondomeko ya Old Mutual , Rosaline Kapadzola , wayamikira maphunziro olimbikitsa kusunga chuma komanso kukonzekera za Imfa.Mayiyu, yemwe ndi namwino M’boma la Chikwawa, wati ndondomeko yokhuza za Imfa, idamukodola mtima pamene adataya Mchimwene wake .Ndipo mchemwali wake adali atachita kale ubwenzi ndi Old Mutual, kudzera mu Mthunzi Funeral Service. Rosaline ,wati pamene mayi awo adamwalira, adathandizidwa moyenerera pa mwambo onse wa maliro.
Wezi Thondoya, yemwe ndi mdindo wolemba ndi kuchotsa anthu pa ntchito ku Kampani ya Illovo, wathiriranso mang’ombe pa chithandizo chomwe adapeza mayi awo atamwalira. Malingana ndi Thondoya, adachita chidwi ndi ukadawulo omwe a Mthunzi Funeral Service adawonetsa poyendetsa mwambo wa zovuta kuchoka ku Lilongwe kukafika ku Rumphi.
Bernard Chiluzi, wati ndalama siyamasewera ndipo imafunika kuyigwiritsa ntchito bwino. ” Ndalama siyamasewera, mkulu wa kampani amatha kubwereka ndalama kwa wantchito wammusi kwambiri pa ntchito “. Chiluzi wapempha anthu kulumikizitsa ngongole ndi masomphenya awo.
Mphunzitsi-yu, walimbikitsa anthu omwe ali ndi ngongole kuti asadziphe koma kubweza maka kuyambira iyo ya chiwongola dzanja kwambiri, komanso kukambirana ndi mwini ngongole pa ndondomeko yobwezera ngongoleyo kuti ayimitse chiwongola dzanja.
Benard Chiluzi ,walangiza anthu kuti asamakhale khumutcha pa tsiku lomwe amalandira ndalama ku ntchito kokha ayi.
Amene wadzala , amakolola. Yambani kudzala ndalama zanu lero.