MALAWI AKUSOWA KAGANIZIDWE KA NGWIRO
Written by Kradio on September 5, 2024
Kwa nthawi yaitali anthu mdziko muno akhala akututumuka ndi imfa zokudza pongodzipha.A Joseph Maseke, katswiri pa nkhani yoona za thanzi la mmalingaliro watambasula kuti kaganizidwe ka ngwiro ndi kukhala osakhumudwa kapena nkhawa mmalingaliro.
A Maseke atchula ma ubwenzi amene achinyamata amakhala nawo kuti ali ndi kuthekera kwa kukulu kokhudza kaganizidwe ka ngwiro. Katswiri-yu wadandaula kuti ngati dziko sitikuchita bwino kumbali yolimbikitsa kaganizidwe kangwiro. “Zina zikuyenda bwino za kaganizidwe ka ngwiro komabe , zambiri za kaganizidwe kangwiro sizikuyenda”.
Mkulu owona za thanzi la mmalingaliro-yu wati mavuto a zachuma,mchitidwe ochita Juga(Gambling & Betting),Nkhawa,kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo zakolezera kusowa kwa kaganizidwe ka ngwiro.
Katswiri-yu wati pali nkhawa yaikulu yodzakwaniritsa Maloto a Malawi 2063 ngati dziko lino siririmbika ku nkhani ya kaganizidwe ka ngwiro.Chitukuko cha Malawi 2063 chikudalira kudzakwaniritsidwa ndi anthu a Malingaliro a thanzi.”Maganizo a ngwiro ndi nsanamira yodzakwaniritsira Maloto a Malawi 2063″.
Maseke wati kudzipha ndi mchitidwe umene ukuvuta mdziko muno .”Lipoti la Police likusonyeza kuti Chiwerengero cha anthu omwe adzipha chaka chino ndichochuluka kawiri kusiyana ndi chiwerengero cha anthu omwe adadzipha chaka chatha”.
Katswiri-yu wadzudzula mchitidwe osayankhulana kaamba kotanganidwa ndi kugwiritsa ntchito Luso la makolo ngati Lamya.”Makolo ndi ana samayankhulana chifukwa aliyense amakhala watanganidwa pa Lamya yake ngakhale kuti anthuwo ali pa malo amodzi”.
Malingana ndi a Joseph Maseke , ati ngati Boma zambiri zokhudza kuthana ndi mavuto a kaganizidwe ka ngwiro zikuvuta kumbali yophunzitsa anthu za kuipa kodzipha.Iwo ayamikira Mipingo ndi mabungwe ena omwe akuyesetsa kuphunzitsa anthu za kuopsa kwa mchitidwe ongodzipha. “Achinyamata alero ndiye atsogoleri a mawa ndipo ngati ali osokonekera mmaganizo zidzachititsa kuti mavuto okhazikika mu zinthu zosokoneza kaganizidwe ka ngwiro apitirire”.
Mkulu-yu wapempha adindo,Makolo ndi anthu ena kuti aphunzitse achinyamata zokhudza ubwino ndi kuipa kwa Luso la makono. Iye wapemphanso achinyamata omwe atitimira mu vuto lakusowa malingaliro a ngwiro akuyenera kusintha pozindikira kuri Moyo-wu ndi kamodzi.Ngati akukanika kusintha paokha apeze akatswiri oona za thanzi la mmalingaliro kuti athandizidwe.
Malingana ndi lipoti la Police, anthu okwana 281 adzipha mdziko muno kuyambira Mmwezi wa January kufika Mwezi wa June Chaka chino(2024), kaamba ka vuto la kusowa thanzi mmalingaliro .