Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

MALAWI AKUVUTIKA KUSAMALIRA ZA CHILENGEDWE

Written by on September 5, 2024

Munthu umafika ponyasitsa nkhope pamene maso ako akumanizana ndi zinyalala mmizinda ndi mma town a dziko lino.Bungwe la Clean Cities Project lidabadwa ndi cholinga chofuna kulimbikitsa  kusamalira chirengedwe, kusintha kwa Nyengo ndi ukhondo.

Mtsogoleri wa Bungwe-li, Martin Manyozo  wati  iwo monga achinyamata ndi anthu okonda dziko lino kotero kuti  akufuna kuthandizira kusintha mizinda yathu malingana ndi Maloto a Malawi 2063,kuti kutsogolo kuno anthu azidzaona dziko lino ngati mayiko monga Denmark ndi Rwanda amene ndi mayiko aukhondo kwambiri pa dziko lapansi.”Mukaona mmizinda yathu mumakhala umve osiyanasiyana. Mwachitsanzo,malingana ndi kukufuku wa Bungwe la United Nations Environmental programme, lidapeza kuti dziko lino limakhala ndi zinyalala zopyola Matani 280 pa Chaka zomwe sizimatayidwa. Kotero nchifukwa amakhala patsogolo kulimbikitsa ukhondo kuti Matenda a Cholera apewedwe.”

Manyozo wati Bungwe lawo liri ndi Ndondomeko yotchedwa Climate Shield,yomwe cholinga chake ndi kuthana ndi Ngozi za Chirengedwe zogwa mwa dzidzidzi ngati kusefukira kwa Madzi.Iwo amaphunzitsanso ana a Sukulu ndi ena oyendayenda  kupanga Zibangiri ndi zinthu zina zochokera ku zinyalala mu ndondomeko yotchedwa Waste to art.

Kumbali yake Mkulu oyang’anira kusamalira za Chirengedwe pogwiritsa ntchito Luso la Makono(Digital performance ) Lloyd Chunga wati munthu ayenera kusamalira zinyalala.”Chinyalala chimasangalatsa ukamaponya pa khomo la mzako,koma wina akaponya  chinyalala pa khomo kapena pa Malo  pako imeneyo ndi Nkhondo “.

Bungwe-ri likugwira ntchito ndi mabungwe ang’onoang’ono a  achinyamata ngati Youth Corner Malawi ya ku Mtandile, Nyasi Mayazi Movement ya ku 25, ku Mchesi,ku Likuni ,ku 23,Sukulu ya Livingstonia ndi Lake Malawi pofuna kulimbikitsa adindo ndi anthu wamba kuti mizinda yathu ikhale ya ukhondo.

Atsogoleri a Clean Cities Project -wa ati kuthekera kulipo kobwezeretsa Chirengedwe mchimmake. Iwo atchula mfundo zokuti Mayiko amene amapanga utsi oyipa umene umaononga Mitambo azithandiza Mayiko osauka kuti asamakhudzike ndi zotsatira za kusintha kwa Nyengo.China ndi kusiya kudula Mitengo mwa chisawawa . Mamulumuzanawa anafotokozanso kuti akulimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito Makala opangidwa kuchokera ku Zinyalala ndi cholinga chothandiza anthu amene amagwiritsa ntchito Makala ochokera ku Mitengo kuti asiye kutero.

Iwo ayamikira Boma kudzera mu Nthambi yoona za Chirengedwe ndi Makhonsolo pogwira nawo ntchito. Komabe atsogoleri-wa ati pali kunyalanyaza kwa adindo pofuna kukwaniritsa Ndondomeko zolimbikitsa Ukhondo mmizinda ya Dziko lino.

Dziko la Malawi lakhala likukanthidwa ndi Ngozi monga Kusefukira kwa Madzi, Matenda a Cholera, kuchedwa kulandira Mvula ,Ng’amba ndi zina zambiri zomwe zaononga katundu ndi Miyoyo ya anthu.


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist