MALAWI ASATAYE NTHAWI NDI ULIMI WA MAKOLO
Written by Kradio on May 26, 2025
Posachedwapa njala ikukodolerani ku zakudya zofuma ku Ulimi. Si Ulimi onse omwe umabweretsa zokolola zochuluka koma wa makono. Katswiri pa nkhani za chuma ndi ulimi, Dr. Felix Jumbe,wafotokoza kuti ulimi wa Makomo ndi Ulimi wa dongosolo,umene umapereka ndalama zokhala chuma cha dziko.
“Tikamati dziko la Malawi ndi losawuka timanena inu pa Banja lanu, tikamatinso Malawi ndi wolemera, timanena inu pa Banja po. Osati Boma n’losauka. Nchifukwa chake anthu ogwira ntchito M’boma, amanona”. Watero, Dr Jumbe.
Katswiri-yu wafotokoza kuti ulimi wa chikhalidwe (wamakolo) ndi umene umatipatsa zinthu zochepa posiyamitsa ndi ulimi wamakono , omwe umabweretsa zokolola zochuluka pa malo ochepa. Dr. Felix Jumbe, wadandaula kuti alimi ambiri mdziko muno akuchita ulimi wa makolo, zomwe zikuyika dziko lino pa chiopsyezo cha Umphawi.
Mkuluyu, wati ngati Njira komanso Mbewu zamakono zingamagwiritsidwe ntchito pa maanja ambiri zitha kuchititsa dziko lino kukhala ndi zokolola zochuluka.
Pothirirapo ndemanga pa nkhani ya mavuto omwe alimi ang’onoang’ono akukumana nawo, Katswiri-yu, wati vuto lalikulu ndi dzina lomwe lidaperekedwa kwa alimiwa. “Anthuwa adakhazikitsidwa m’gulu la zochitika zochepa( small holder farmers), Chiwongo chi zotsatira zake ndi umphawi. Dr. Jumbe, wapereka chitsanzo cha maphunziro ponena kuti anthu ambiri ophunzira amangoganiza za ntchito ya mu ofesi osati ulimi. Iye, watchulaponso kuchepa kwa maphunziro a alimi ang’onoang’ono kuphatikizaponso kuthetsedwa kwa magulu ( club) kuti ndi ena mwa mavuto omwe alimiwa akukumana nawo.
“Dziko lino kuti lidzachite bwino pa Ulimi, Mtsogoleri wa dziko lino ndi amene akuyenera kukhala patsogolo. Mukadandifunsa kuti ndikadakhala mtsogoleri wa dziko lino, ndikadatha kulumikizitsa alimi ku Misika ya kunja, osati Nduna”. Dr. Felix Jumbe, wayankha motero atafunsidwa kuti akadakhala Nduna ya za Ulimi, akadachita zotani pofuna kutukula Ulimi mdziko muno. Iye, sanapsyatire mawu ponena kuti Nduna imachotsedwa ntchito ikakhala ndi ndondomeko za bwino za momwe angachitire ntchito yake ngati Nduna ya za Ulimi.
Dr. Felix Jumbe, wakhazikika pa Chikhalidwe, kuti ndi chomwe chikuwononga ntchito zotukula dziko lino.Iye, wadzudzula anthu komanso mabungwe omwe amalimbikitsa Ulimi wa makolo kuti akuyika dziko lino pa umphawi wa dzaoneni.
Katswiri-yu, wadandaula kuti dziko lino likhala pa Njala yaikulu kaamba kokakamira ulimi wa Makolo. Dr. Jumbe, wati anthu pafupifupi 3 ndi 4 Million, ali pa chiopsyezo cha Njala.
Kuyambira mzaka za mma 2000,Dziko lino lakhala pa Ndondomeko ya Starter Pack, FISD, AIP pofuna kuthandizira ulimi kupita pa tsogolo, koma lero lino angakhale kudya katatu pa tsiku sikukutheka kaamba kolowetsa Ndale ku Ulimi.Malawi imadalira Ulimi wa Mbewu monga Fodya, Chimanga, Soya ndi Thonje pongotchulapo zochepa chabe.