MALAWI WAKHALA PA CHUMA CHOBISIKA
Written by Kradio on July 9, 2024
Malonda ambiri mdziko muno amayamba akwezedwa pa Sikelo asanasinthanitsidwe ndi ndalama. Ndi Malonda amodzi okha a Golide omwe atati akwezedwa pa Sikelo atha kusinthanitsidwa ndi 150 Million Malawi Kwacha pa Kilogram imodzi.Miyala ya Mtengo wapatali ndiyo ili ndi kuthekera koonjola anthu pa umphawi wa dzaoneni.
Malingana ndi kafukufuku dziko la Malawi ndi dziko losaukitsitsa kwambiri pano pa dziko lapansi. Mmodzi mwa akatswiri pa Nkhani ya zamiyala ya mtengo wapatali a Timothy Ada Mbewa wati, “Malawi ali ndi Miyala ya mtengo wa patali ,chuma china ndi zokopa alendo ndi Ulimi”. Tikaona kumbali yokopa alendo ,dziko lino likuchita bwino ndithu koma tiri ndi kuthekera kochita koposa. Tikapita ku Ulimi,dziko lino limadalira kwambiri ulimi wa fodya. Ada Mbewa, apereka chitsanzo cha dziko la Democratic Republic of Congo ngati dziko limodzi lomwe Chuma chake sichimabwerera mbuyo popeza iwo amadalira kwambiri kugulitsa Miyala ya Mtengo wa patali ngakhale liri dziko lomwe liri pa Nkhondo kwa nthawi ya itali.
Malingana ndi a Mbewa, dziko la Malawi ndilosavuta kutukuka ndi malonda a Miyala ya Mtengo wa patali. 95% ya anthu mdziko mumo amakhala akudalira ntchito za mma ofesi zomwe ndizodandaulitsa kwambiri. Katswiriyu wapempha Boma kuti liyike chidwi chake polimbikitsa malonda a miyala ya mtengo wapatali kuti chuma cha dziko lino chitukuke.
Mayiko monga China,South Africa, Mozambique,Tanzania ndi Zambia anatukuka ndi ntchito za migodi pochita Malonda a Miyala ya mtengo wa patali.