Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

MALAWI WATAKASA NTCHITO ZOKOPA ALENDO

Written by on July 31, 2024

Mneneri mu nthambi ya unduna wa zokopa alendo ndi zachirengedwe, a Joseph Nkosi ati dziko la Malawi likupita patsogolo potukula ntchito yosamalrira malo osungira Nyama za kutchire ndi zachirengedwe zomwe ziri ndi kuthekera kotukula dziko lino pa Chuma.

Polankhula mu Program ya “Touring Malawi”  pa wailesi ya Kasupe , a Nkosi afotokoza kuti malo osungira Nyama za kutchire ndi chirengedwe ndiofunika kwambiri chifukwa amathandiza anthu pa umunthu , kusunga mitengo ya chirengedwe komanso dziko kuti lipeze Ndalama ya kunja(foreign currency).

“Ifeyo ngati a Malawi tiri ndi Malo osungira Nyama za kutchire ndi zachirengedwe abwino kwambiri omwe ali ndi zinthu zomwe kwina sizimapezeka.Mwachitsanzo ,Liwonde National park kapena Majete Game Reserve , ndi malo abwino omwe Nyama zakutchire zimapezeka mu Malo ake enieni omwe sizimasokonezedwa ndi gulu la anthu ndipo anthu ndiamene amazindikira kuti iwo ndi alendo mmalo-wa zomwe ndizosiyana ndi Malo a Mmaiko ena. Tiri ndi Nyama zikuluzikulu (the big five),Nyama monga Njobvu,Njati Kambuku,ndi Mkango.Izi zimathandizira kuti dziko lino lidzikopa alendo,  anatero Mneneri wa Nthambi yoona za Chirengedwe-yu.

Pothirirapo ndemanga pa ntchito yosamutsa Nyama kuchoka ku Malo ena kupititsa ku Malo ena zomwe zakhala zikuchitika mdziko lino, a Nkosi ati Ntchitoyi ndiyopitirira ndicholinga chokuti malo onse osungira Nyama-zi akhale ndi Nyama zochuluka kuti anthu asamayende mtunda wautali akafuna kuona Nyama zosiyanasiyana.

Kumbali ya chitetezo cha Nyama, Mneneri mu undunawu wadandaula ndi anthu(amalawi ndi ammaiko ena) omwe amachita mchitidwe osaka ndikupha nyama zachirengedwe ndipo ati ngati unduna akuyesetsa kugwira ntchito ndi anthu okhala mozungulira malo osungira Nyama.

“Timapereka mbuzi ku madera a anthu okhala mozungulira malo osungira Nyama kuti ikaswa adzipatsana komanso ulimi wa Njuchi omwe timawapezera Misika yogulitsa Uchi,tirinso ndi agalu ophunzitsidwa bwino mmalo olowera ndi kutulukira mdziko muno omwe amanunkhiza ngati munthu watenga Nyama zakutchire ndipo tikugwiranso ntchito ndi Mabwalo oweruza Milandu.”

“Pakatipa Ngaka (pangolin) ndi Nyama yomwe yakhala ikubedwa mmalo osungira Nyama zakutchire ndipo a Nkosi ati bvuto anthu samamvetsa za kufunika kwa Ngaka,  “ Iyi ndi Nyama yofunika kwambiri pobwezeretsa Nthaka, iyo imatembenuza Nthaka ndikupanga manyowa.Tithokoze kwambiri anthu omwe anatengapo mbali pophunzitsa anthu za kufunika kwa ngaka yomwe mmaiko ambiri kulibe ndipo ife tiri nayo. Kupezeka ndi Ngaka mdziko muno ndi Mulandu.”

“Ngati unduna ati akugwira ntchito limodzi ndi maiko ena omwe ndi abwenzi pa Chitukuko. Bungwe la African National Parks lakhala bwenzi la dziko lino pothandizira kusamutsa nyama kupititsa komwe kulibe nyama zambiri ndiponso akuthandizira kusamalira Malo osungira Nyama ndi Malo ogona alendo omwe amapezeka Mmalo ochititsa chidwi-wa.”

“Ndithokoze abwenzi pa Chitukuko ndi anthu okhala mozungulira Malo osungira Nyama za kutchire omwe akhala akutithandiza mu njira zosiyanasiyana”, Anatero a Nkosi. Iwo apempha a Malawi kuti agwire limodzi ntchito ndi undunawu pofuna kusamalira Nyama za kutchire ndi Chirengedwe. Dziko la Malawi liri ndi Malo osungira Nyama zakutchire asanu ndi anayi (Nyika National Park,Vwaza Game Reserve,Nkhotakota Game Reserve,Kasungu National Park, Lake Malawi National Park,Liwonde National Park,Majete Game Reserve,Lengwe National Park ndi Mwabvi Game Reserve). Mdziko muno tsopano muli chiwerengero cha nyama zakutchire chochuluka.


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist