Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

MULI CHUMA MU ZINYALALA

Written by on September 5, 2024

Sabata silimatha anthu okhala Mmizinda ndi mma town a Dziko lino asadaone zibinyira za zinyalala mphepete mwa Misewu zikudikira kunyamulidwa kuti zipite ku Mtaya.

A Stephen Chiunjira ndi nkulu wa  Bungwe la Our World international ,yomwe imapanga zosintha zinyalala kuti zikhale Manyowa ndi zinthu zina zosiyanasiyana ku Kawale 2, mu Mzinda wa Lilongwe . Iwo ati amasintha kaganizidwe ka anthu kuti adzigwiritsa ntchito zinyalala kupangira Manyowa ndi zinthu zina .

Bungweli likutukula miyoyo ya anthu okhala mozungulira dera-li kupyolera mu ntchito zake.”Ifeyo tiri ndi Ndondomeko Msukulu zosiyanasiyana  kumene timaphunzitsa ana kaganizidwe kabwino  ka momwe tingasinthire zinyalala. Timachotsanso zinyalala mmalo osiyanasiyana pogwira ntchito limodzi ndi Mipingo,ma Kampani ndi  ma Bungwe. Timagwiranso ntchitoyi limodzi ndi Mafumu.Panopa tiri ndi Ndondomeko yoti tifikire akaidi omwe alipafupi kutuluka, kuti tidzawapatse ngongole kuti adzichitira Geni zosiyanasiyana ,zonsezi zikuchokera mu zinyalala.Tirinso ndi mpikisano omwe umatchedwa Cleanest Greenest Lilongwe City, umene ukulimbikitsa ukhondo Nyumba,Mmalo ochitira Malonda ,Mzipatala ndi malo ena. Pamapeto pake anthu amalandira Mphoto zosiyanasiyana”. Anafotokoza a Chiunjira.

Mkuluyu wati  ngakhale akukwanitsa kuchita izi, akukumana ndi mavuto osiyanasiyana maka kumbali yosowa thandizo potengera kuti Bungwe lawo silopanga phindu. Kaganizidwe ka anthu kuti asinthe momwe angapangire ndi Zinyalala.

“Ngati Bungwe, anthu ambiri apindura ndi Manyowa. Anthu akumabwera kudzaphunzira kapangidwe ka Manyowa enanso amadzatigula, thumba lolemera 50 Kilogalamu timaligulitsa pa mtengo wa K10,000. Ma Kampani ena amatifikira kuti tiwathandize kusamala Zinyalala”. Anafotokoza  a Stephe Chiunjira .

Iwo ayamikira Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe, United Nations Development Program ndi mabungwe omwe nthawi zina amawagwira dzanja mu zinthu zosiyanasiyana komanso anthu ,amene amabweretsa Zinyalala ku Bungwe lawo .

A Chiunjira apempha anthu kuti agwirire ntchito limodzi posamalira Zinyalala kuti zipindulire onse.

Kumalawi kuno mchitidwe ongotata Zinyalala mmalo osayenera ngati mmitsinje ndi mphepete mwa Msewu ndiochuluka kwambiri zomwe zimatha kupereka Chiopsezo ku Miyoyo ya anthu ndi zachilengedwe zina.


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist