MWINI NDALAMA
Written by Kradio on October 28, 2024
Pa zinthu zomwe munthu amaganizira tsiku ndi tsiku ndalama imakhala pa mndandanda wa zinthu zoganiziridwa. Kaganizidwe kangwiro nako ndi kofunikira pa nkhani ya ndalama. Benard ChiluzI, yemwe ndi Mkulu oyang’ana za maphunziro abwino a kayendetsedwe ka chuma ,wati kuganiza molungama ndi kaganizidwe komwe sikungamupezetse munthu mavuto kapena ndi kuganiza mu njira ina chifukwa cha zinthu zimene munthu akuwona, kumva ngakhale ku nunkhiza, kuganiza komwe kungamuthandizire kuti apite patsogolo.
A Chiluzi, atsindika kuti anthu sakusowa ndalama koma anthu alibe ndalama zokwanira zokuti agwiritse ntchito pokhala ndi zinthu zimene amafuna.”Vuto lalikulu padakalipano ndi lakuti anthu akusowa ndalama zokuti agwiritse ntchito pa zinthu zimene akufuna”.
A Chiluzi, apereka chitsanzo cha transformer kuti Boma limaika transformer mdera lanu chomwe ndi chitukuko chagulu, koma zimatengera munthu kukoketsa magetsi Nyumba mwake. “Chitukuko cha Maiko chimakhala cha gulu, zitengera munthu kukoketsa nthambo ya Magetsi, kuti akhale nawo Magetsi-wo”. Mkuluyu, watero pofuna kumveketsa kuti munthu payekha ayenera kuchitapo kanthu kuti apeze ndalama.
“Anthu a ndalama samawayimbira likhweru. Koma ukakhala opanda ndalama , umaitanidwa ndi likhweru”. Chiluzi ,watchula chizindikirochi.
Mkuluyu, watsutsa kuti ndalama si Satana.” Ikadakhala kuti Ndalama ndi Satana, bwenzi umphawi uli chiphasò chopitira kumwamba”. Mphunzitsi pa nkhani ya kayendetsedwe kabwino ka chuma-yu,watero.
Chiluzi, wati anthu amene amaganiza bwino komanso ali ndi ndalama, samadzidzimuka ndi zinthu ndipo waonjezera kuti ndalama zimadana ndi Phuma.” Tiyerekeze kuti ku Ofesi ,mumalandira uthenga wa pa lamya kuti ndalama zalowa, wina amatutumuka nkumakuwa kuti ‘zalowa!zalowa ‘ “.
Mkulu ophunzitsa kayendetsedwe kabwino ka chuma-yu , wati anthu ambiri amaiwala kuti adzakalamba ndipo samazikonzekeretsa poikiza Ndalama zokuti zidzawathandizire ku zaka za kumapeto a Moyo wawo, atatha kugwira ntchito. Iye, wapempha anthu kuti asamalamuliridwe ndi ndalama koma munthu adzilamulira ndalama.
Mkuluyu, wati njira yabwino imene munthu oganiza mwa ngwiro angapezere ndalama, ndi nthawi imene zinthu zavuta mdziko. Iye wapereka chitsanzo cha madobadoba, kuti amapanga ndalama pamene mdziko muli njala. Mkuluyu, wapitiriza kunena kuti anthu akachita ngozi, eni kampani zokoka galimoto zomwe zachita ngozi amasangalala kuti apeza mopanga ndalama. A Chiluzi , anena izi pofuna kutsindika kuti munthu akuyenera kupeza njira yothetsera mavuto a mzake, uku akupanga ndalama.
A Bernard Chiluzi, apempha anthu kuti adziikiza ndalama uku akuzichulukitsa.”kubadwa osauka sikusankha koma kudzafa osauka ndi chisankho”. Iye, watsindika.
Malingana ndi bank yayikulu pa dziko lonse lapansi (World Bank), idapenekera kuti chuma cha dziko la Malawi, chikula ndi ma peresenti awiri okha ndipo umphawi upitirira kupita pa tsogolo.