NYENGO YA MDZIKO LA MALAWI YASANDULIKA
Written by Kradio on December 27, 2024
Zovala zomwe anthu timavala zimagwirizana ndi nyengo, ntchito zathu zimene zimachitika malingana ndi Nyengo. Tikawunikira nyengo ya mvula kuno kwathu ku Malawi ,nayo idasintha.
Chifundo Dalireni , yemwe ndi mmodzi mwa akatakwe a zachirengedwe watsimikiza kuti nyengo idasintha.”Nyengo idasintha pafupifupi pa dziko lonse lapansi”. Katswiriyu wafotokoza kuti kudula mitengo, kutulutsa utsi kwambiri ku ma fakitale ndi zina mwa njira zomwe zakolezera kusintha kwa nyengo.
Dalireni, wadandaula kuti ngati dziko nkhani yosamalira za chilengedwe zikutivuta . “Anthu tikudula mitengo mwa chisawawa, ndipo kuti mitengo idulidwe ndi chifukwanso chakuti anthu tikuchulukana. Kale kudalibe Area 49 komanso Bwalo la ndege la chileka kudalibe nyumba za anthu ogwira ntchito. Koma lero kuli nyumba zambiri ndipo kudula mitengo kukuchitika komanso anthu akutsegula ma Fakitale”.
Namandwa pa nkhani za chilengedwe yu ,wavomereza kuti dziko lino lipitirira kukhala pa chiopyezo chokudza kaamba ka kusintha kwa nyengo ngati anthu tingapitirize kusasamala za chilengedwe. Mkuluyu, wati Boma palokha siringakwanitse kusamalira mitengo. Iye, wapempha anthu kuti aliyense atengepo gawo posamalira mitengo. Dalireni ,wachenjeza anthu kuti asamalime ndi kumanga nyumba kufupi ndi kumitsinje komanso kuotchya makala.
Kupezeka kwa zophikira za makono ngati Gas, Dalireni wati iyi ndi njira imodzi yosonyeza kuti dziko likuyesetsa kulimbana ndi mchitidwe owotchya makala.”Sitinganene kuti tikuchita bwino koma tikuyesetsa. Mukayenda mma town pali Malo ambiri amene akugulitsa zophikira za makono ndi Gas. Pali project ya dziko la America ndi dziko la Britain, yotchedwa modern cooking, chitukuko chimenechi ncha mma town kuti anthu asamakhale ndi maganizo akuti makala ndi otchipa kuposa magetsi kapena gas”.
Chifundo, wamema anthu mdziko muno kuti adzigwiritsa ntchito gas pophika. Kumbali ya kuopsya kogwiritsa ntchito gas ngati momwe ena amayenera, Katswiriyu wati anthu amaphunzitsidwa bwinobwino momwe angagwiritsire ntchito gas.
Dalireni, wanena poyera kuti anthu a ndale amakolezera mchitidwe odula mitengo mwa chisawawa powateteza anthu ndi cholinga chofuna kukhala okoma kwa anthuwo.
Pa nkhani yogwiritsa ntchito mapepala a plastic opyapyala, Katswiri wa zachirengedwe-yu wapempha a Bwalo la milandu , kuti liyesetse kuthetsa mchitidwe opanga ma plastic opyapyala. Chifundo wafotokoza kuti mapepala opyapyala amatenga zaka zoposa zana limodzi kuti awole kotero ali ndi kuthekera koononga nthaka komanso kuyambitsa nthenda ya cancer. “Pa Kenya pomwepa kuti munthu watsika ndege, amanena kuti ngati uli ndi mapepala opyapyala amakusiyitsa nkukugulitsa ena oyenerera”.
Chifundo, wapempha kuti anthu athandize luso la makono pothana ndi nkhani ya mapepala opyapyala. Katswiriyu wapemphanso amalawi kuti aliyense atengepo mbali posamalira chilengedwe.
Dziko la Malawi lakhala likukumana ndi ngozi zokugwa kaamba ka kusintha kwa nyengo. Mwachitsanzo, mchaka cha 2023, miyanda miyanda yaanthu idapululuka kaamba ka namondwe wotchedwa Freddy yemwe adaomba mchigawo cha kumwera kwa dziko lino.