ZIPHUPHU NDI KATANGALE ZAIMITSA CHITUKUKO CHA DZIKO
Written by Kradio on August 2, 2024
Mkhalakale pa Ndale a Jessey Kabwira ,apempha Bungwe lothana ndi Katangale ndi Ziphuphu la ACB,kuti lichitepo kanthu pofufuza ndi kupereka chilango kwa anthu omwe amachita katangale ponena kuti dzikoli likunyeka pa moto kaamba ka mchitidwe wu.
Kabwira wati mdani wa mkulu wa utsogoleri wabwino ndi kudzikonda komwe kumachititsa kuti atsogeri azidzikundikira chuma. Utsogoleri umayenera kuimira anthu ndi kuonetsetsa momwe zinthu zikuyendera osati kudziremeretsa. Kusankha pothana ndi katangale pa zifukwa za chibale kapena ndale ndi zina zomwe zikukolezera mavuto omwe dzikoli likukumana nawo.
Phungu wa kale wa kumpoto cha kumadzulo kwa boma la Salima yu wati ku ndale,mmabungwe a boma ndi ena kuli katangale wa mnanu.Ndipo iwo apempha adindo mmagawo osiyanasiyana kuti adzikonda anthu osauka omwe amakhudzika kwambiri ndi ziganizo zomwe adindowa amapanga.
Poonjezerapo Kabwira wapempha mafumu ndi bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana la NICE, kuti achirimike kuphunzitsa anthu za kuipa kwa Ziphuphu ndi Katangale.
Kwa nthawi yoyamba yemwe adali mkulu wa kale wa Bungwe la ACB mayi Martha Chizuma adamangidwapo ali mkatikati mofufuza milandu ikuluikulu ya Katangale. Kafukufuku wa mdandanda wa maiko othana ndi katangale akuonetsa kuti dziko la Malawi liri ndi ma point 30 pa 100.