Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

MARY CHILIMA WAPEMPHA KAFUKUFUKU WAPADERA

Written by on October 4, 2024

Mdima wa ndiwe yani  wokhudza zomwe zidachitika kuti ndege yomwe idanyamula wachiwiri wa kale wa  Mtsogoleri wa dziko lino Malemu Dr Saulosi Klaus Chilima , udakakodolabe Mitsinje ya misonzi kwa a Mary Chilima ,omwe  pa 29 September 2024  adalemba pa tsamba la mchezo la facebook  kupempha  okhuzidwa onse kuti awathandize kupanga kafukufuku wapadera. Iwo adajambulitsa  pa malo pomwe ndenge yomwe idanyamula amuna awo idagwera pamene amakumbukira ulendo wawo wa banja ndi Malemuwa . Mayi Mary Chilima ,apempha a Malawi kuti pakhazikitsidwe bungwe lomwe lichite kauniuni  pa zomwe zidachitika mwatsatane tsatane kuchoka pa 10 june kufika pa 11 june  tsiku limene ndege idapezeka kuti yagwa.

Katswiri woyankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana a George Phiri , wayikira kumbuyo ganizoli ponena kuti ndizoyenera kutero. “kwa ineyo ndikuona kuti ndi choyenera chifukwa chichitikireni ngozi ija kafukufuku amene wachitika sadaonetse chomwe chidachitika kuti ndege igwe komanso anthu onse afe. A Malawi komanso mkazi wa Malemu Saulos Chilima  akuyenera kudziwa chomwe chidachitika kwa a Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu ”.  Phiri, watero.

A George Phiri ,apempha Boma kuti likuyenera kukhazikitsa kafukufuku wapadera woyima payekha (independent commission of Inquiry)  kuti akubanja ndiye adzalengeze zotsatira za kafukufuku yu. A Phiri  avomereza kuti a Mary Chilima sali okhutitsidwa ndi kafukufuku yemwe wachitikapo kale ndi gulu la akatswiri owona zangozi ya Ndege la ku Germany, la German Federal Bureau of Aircraft Accident Investigation  . ” Ngati a Malawi sakumvetsa za zimene  zidachitika ku Chikangawa , nawo a Mary  sakumvetsetsa kuti vuto la Ndege linali  lotani chifukwa Ndege siidapse, chidachitika ndi chani kuti anthu adzikasaka ndege komwe siidagwere?”.  Phiri watero akudabwa.

Phiri watsindika kuti Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ,wachedwa kukhazikitsa kafukufuku wapadera.” Tikhoza kunena kuti Mtsogoleri wadziko lino wachedwa pamene padutsa miyezi itatu asadakhazikitse kafukufuku mpakana pano chigwereni ndege. Ngakhale Mtsogoleri wa dziko lino sadapite pa malo omwe adachitikira Ngozi ya ndege,zikuonetseratu kuti alibe chidwi”. Komabe  mkuluyu wati ngakhale kafukufuku angakhazikitsidwe pakhale kusintha kuti zomwe kafukufuku apeze akhale ndi phindu. Iye anapitiriza kunena kuti Boma lisamakhalire zinthu za kafukufuku wapadera.

A George Phiri , avomereza kuti ndale zimalowerera pa kafukufuku.” Ndale zimalowererapo chifukwa amakhazikitsa kafukufuku ameneyu ndi atsogoleri a ndale  omwenso amalandira lipoti ndi kulengeza zotsatira za kafukufuku”. Mkuluyu wati akubanja , asilikali ndi anthu ena okhudzidwa asakhale mu gulu lomwe lichite kafukufuku kuti zotsatira zake zidzakhale zovomerezeka.

Phiri wamema a Malawi kuti aphunzire kumafunsa atsogoleri pa zinthu ngati zimenezi ndipo ngati pangakhale kunyalanyaza  njira zina zikhalepo kuti amene wakhalira lipoti adzibweza Ndalama zonse zomwe zagwiritsidwa ntchito pochitira kafukufuku.

Pa 10 June 2024,Dziko la Malawi lidachita tsembwe ndi  kusowa kwa ndege ya a silikali yomwe idanyamula  wachiwiri wakale wa  Mtsogoleri wa dziko lino yemwenso adali Mtsogoleri wa Chipani cha United Transformation Movement (UTM) ndi anthu ena asanu ndi atatu. Ndege yi idapezeka mu nkhalango Ya Chikangawa M’boma la Mzimba

 

Dr Saulos Klaus Chilima adali katswiri pa nkhani za Chuma komanso wa ndale yemwe adakhalapo ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino kuchokera mchaka cha 2014 kufikira 2019 komanso 2020 kufikira nthawi ya imfa yawo mu 2024.


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist