PHINDU LA MAPHUNZIRO A CHUMA KU MALAWI
Written by Kradio on December 27, 2024
Chuma ndi chinthu chimene chimafunikira kwambiri pa moyo wa munthu aliyense posatengera komwe munthu amachokera. Maphunziro a nkhani za chuma kuno kwathu ndi mnyanga wa njobvu.
Katswiri pa nkhani ya zachuma,Innocent Banda watsindika kuti muli phindu mma phunziro a nkhani za chuma”Maphunziro a zachuma ali ndi phindu pa munthu payekha chifukwa Ndalama-zo amazipeza ndi munthu”.
Banda wafotokoza kuti munthu ukakhala ndi luso,luntha ndi ukadaulo pa nkhani za chuma umpanga ziganizo zoyenerera,Kupanga dongosolo la zinthu zoyenera kugula ndi kasungidwe ka chuma komanso kukhala ndi phindu la kagwiritsidwe ntchito kabwino ka Ndalama. Iye, watchulanso kuti phindu lina limene munthu amapeza pa maphunziro a za chuma ndilakuti munthu amatha kuikiza Ndalama zimene ziri ndi kuthekera kolenga ndikulemba ntchito anthu ena komanso munthu umakhala ndi phindu poteteza chuma chako.
Katswiri-yu, wapempha Kampani za Insurance kuti ziyambe kufikira anthu kuti awaphunzitse pa momwe munthu angagwiritsire ntchito chuma chake.”Mwachitsanzo Ku Malawi Juno kuli makampani ambiri a insurance koma ndi a Malawi ochepa kwambiri amene omwe ali ndinmpata otere. Mwachitsanzo ,munthu waikiza bizinezi ya shop,moto wabwera ndipo katundu yense wapsya ndiye kuti palibepo chirichonse chomwe mwapeza koma mukakhala kuti munaphunzitsidwa za insurance, mumakhala ndi ponyamukira kumbali ya chipepeso komanso umakhala ndi mtendere wa mumtima. Banda,wawonjezera kuti ukaphunzitsidwa pa nkhani za chuma, umapewa matenda monga nkhawa.
Innocent, walangiza anthu kuti ngongole timatenga ndicholinga chofuna kuchitira bizinezi komanso kukulitsa bizinezi yomwe munthu alinayo kale osati kukabwereka ndalama ndikudya.”Chofunika pamwamba pa zonse,munthu usanakhale ndi ngongole ukhale ndi ganizo la bizinezi ,udziwe kugula bizinez”.
Banda watchula ndi kupempha anthu kuti adzimvetsera nkhani za chuma pa wailesi ya Kasupe,komanso kuphunzira kuchokera Ku Reserve Bank ya dziko lino ndi mabungwe obwereketsa Ndalama,pa phone yamakono ndi mabungwe omwe siaboma.
Katswiri-yu, wapempha akuluakulu a wailesi ya Kasupe kuti apitirize kudziwitsa anthu za maphunziro a za chuma. Iye, wati ganizo lina ndi kuwonjezera pa maphunziro a za chuma mu ndondomeko ya maphunziro mdziko muno komanso Kukhala nawo pa mikumano ya zachuma.
Pa 23 September,2024, dziko la Malawi lidakhazikitsa ndindomeko zophunzitsira anthu za nkhani ya chuma ndi momwe munthu angapangire ziganizo zoyenerera pa Chuma.