CHIMWEMWE MU ULIMI WA MITENGO
Written by Kradio on February 1, 2025
Zolemba zambiri zimafotokoza kuti ulimi ndi kudzala mbewu komanso kuweta zifuyo pa Malo ogwiritsidwa ntchito ndi anthu. Mutha kututumuka mutamva kuti ulimi ndi kudzala mbewu, kuweta Nyama ndi kubzala mitengo, pozisamalira ndi kuikolola. Musatutumuke ndi zomwe mwamvazi popeza izi ndi zochitika ndithu. Mkulu wa kampani ya Headman Nursery , Elijah Nyirenda ochokera ku Nkhatabay, wafotokoza za ‘malesa’ opezeka mu ulimi wa mitengo.
Iwo ngati Kampani, adaika chidwi popanga pine ndi bluegum wa Makono kaamba ka kusakazika kwa mitengo mu nkhalango ya Chikangawa.”Timapanga mitengo ya pine ndi bluegum wa Makono imene imakula msanga”. Watsindika, Nyirenda.
“Tikudziwa tonse ngati dziko la Malawi takhala tikutumiza mitengo mbuyomu kupita ku Mayiko ena (Tanzania,Uganda,Kenya), koma pano ndi zachisoni kuti mitengo ikuchokera kunja chonsecho mitengo tiri nayo konkuno”. Elijah, wadandaula.
Nkuluyu, wati ubwino wa ulimi wa mitengo muli phindu lamnanu popeza siimathiridwa Feteleza kapena manyowa, siimafuna kuthirira, imakula msanga komanso . Nyirenda wati mitengoyi, imangofuna kupalira poipewetsa ku moto komanso kuitengulira. Iye, wafotokoza kuti ulimiwu umangofuna munda komanso mitengoyo ngati mpamba.
Kampaniyi, yadandaula kaamba koti Boma silikulimbikitsa komanso kuphunzitsa anthu za ulimi wa mitengo omwe ungathandiza kubweretsa Ndalama za Kunja. Mkulu wa Kamaniyi, wapempha Boma kuti liyambe kuphunzitsa anthu za ulimi wa mitengo ya makonoyi , yomwe imakhwima ndi kukololedwa pakatha zaka za pakati pa zosachepera zisanu komanso zosapiririra khumi.
Elijah, wati mtengo wa bluegum umalola nthaka ina iriyonse mdziko muno pamene Mtengo wa Pine ,sikawirikawiri kulola nthaka ya miyala. Mkuluyu watsindika kuti munthu utha upindula kwakukulu ndi ulimiwu . Mwachitsanzo, malo okwana hekitala imodzi,imatulutsa mitengo ya Pine okwana 3100, pamene Mitengo ya bluegum imalowa yokwanira 2700 pa hekitala imodzi.
Kunkhani yopirira poyembekezera kukolola mitengoyi, Nyirenda wati munthu sakuyenera kungopinda manja uku akudikira kukolola koma atha kupitiriza kumagwira ntchito zina uku mitengoyo ikukula kudikira nthawi yokolola.
Elijah, walosera kuti dziko la Malawi, litha kukhala limodzi mwa Maiko opeza Ndalama zochuluka kwambiri kuposa maiko a mu Africa, kudzera mu ulimi wa mitengo-wu(kugulitsa matabwa kunja). Iye, wati zotsatira za Ngozi za chilengedwe zogwa mwa dzidzidzi zobwera chifukwa cha kusintha kwa Nyengo ,kutha kukhala kochepepetsedwa ndi Ulimiwu.
Pankhani ya kulowerera kwa Ndale ku Ulimi osiyanasiyana, Nyirenda ,wati izi ndi zodandaulitsa popeza atsogoleri a Ndale amangokhala ndi Masomphenya a zaka zisanu zokha mmalo moika chitukuko patsogolo. Iye, wapempha a Ndale kuti asamalowerere ndicholinga chobwezera mbuyo chitukuko, ndipo waunikira Boma kuti lisakhazikike potsegula Minda ikuluikulu ndi cholinga chodzala chimanga kapena soya zokha komanso Minda ina idzalidwe mitengo ya makonoyi.
Elijah Nyirenda, wamema anthu mdziko muno kuti ayambe ulimi wa mitengo.
Dziko la Malawi, liri ndi ma Hekitala 90,000 a Nkhalango ku Chikangawa, ndipo mitengo yambiri mu Nkhalangoyi yatha kaamba kodyetsera ziweto, kumanga nyumba zogonamo za malonda, kulima pambali pa zinthu zina zomwe zachepetsa mitengo Mnkhalangoyi.