UBWINO WA KUKONZEKERA POCHITA ZINTHU.
Written by Kradio on February 1, 2025
Pamene mumatsegula tsambali kuti muwerenge nkhaniyi ,ndiri nacho chikhulupiriro kuti munakonzekera.Munthu umakhala kakasi kapena kusowa mtengo ogwira ngati sunakonzekere pakuchita chinachake.Mbusa Vincent Nguluwe, watambasula kukonzekera kuti ndi kukonzekera zinthu zomwe munthu ukufuna kuti uchite kuti ukafikire china chake.
“Kukonzikera kudayamba ndi Mulungu. Genesis 1 ndime ya 1″. Watero , Nguluwe. Mbusayu, wati kukonzekera kumathandizira munthu kukhala ndi chindunji pa zochita, kusakhala mmoyo osokonekera, osadzidzimuka ,kupanga zinthu malo oyenera, mmalo oyenera , pa nthawi yoyenera komanso kwa anthu oyenera . Kuphatikiza app kukonzekera kumathandiza munthu kukachita zinthu zoononga Ndalama pa moyo.
Vincent, wati kusakonzekera kumakhala ndi zotsamwitsa ngati kubalalika , omvetsa chisoni, kusowa mtendere, kusakhala ndi abwenzi okuthandiza pa Masomphenya , kutailira komanso kusakaza Ndalama pa zinthu zopanda phindu.
Mbusa Nguluwe, wapempha anthu kukonzekera mgawo la uzimu( kupemphera), kutumikira Mulungu , gawo la zachuma, maphunziro, kudalitsa anthu ena komanso banja pambali ya magawo ena. Iye, wati anthu asamakhale oduduluka kuononga Ndalama pa chikondwerero cha khrisimasi pounikira kuti kutsogolo kwake kumakhala nkhani za ku munda ndi Ndalama zolipirira sukulu.
Kumbali yoikiza Ndalama mmamangidwe , Vincent, wati ndizofunikira. ” Nyumba ya lendi ingakongole mwa mtundu wanji ndiyamunuwake,siyako”. Mbusayu, walimbikitsanso anthu kuikiza Ndalama pokhala ndi Minda ndi zinthu zina.
Vincent, wadzudzula mchitidwe wa ziwawa umene umachitika mdziko muno ndipo wapempha achinyamata omwe amatengedwa ngati funkha ( engeen ) ya ziwawa pa Ndale, kuti asiye izi.
“Aliyense akuyenera kukhala okonzekera, sizikutengera kuti munthu ukhale ndi maphunziro. Nkhuku zimakonzekera, Nyerere zimakonzekera. Izi ndi mzeru za chirengedwe, zosiyanasiyana ndi za ku Sukulu ” . Wafotokoza motero , Nguluwe.
Mbusayu, wapempha anthu a mtima wa Mataya kuti akuyenera kupanga dongosolo la momwe angadalitsire anthu osati kumangopereka popeza atha kugonandi Njala. Iye, wapitiriza kupempha anthu a pa banja kuti adzikhalira pansi limodzi ndi kuunikira momwe ayendera mchaka cha 2024, ndi kukonzekera momwe angachitire mu Chaka cha 2025. Mbusayu Watsindika kuti kupanga dongosolo la kukonzekera kukutanthauza kuti mzimu akutsogolera.
Vincent, wapempha anthu a Ndale kuti akonzekere kusanamiza amalawi pa zinthu zomwe akudziwa kuti ndi zosatheka.
“Mawu okuti Mulungu achita, samanama. Koma pali ma gawo awiri kuti zinthu ziyende. Mulungu amachita mbali yake , munthunso akuyenera kuchita mbali yake”. Watero, Nguluwe. Iye, wapereka chitsanzo chakuti Mulungu amagwetsa mvula koma Mulungu sangatipitire kumunda kukalima. Ife(anthu) tikuyenera kukalima.
Vincent, wapempha anthu ochita Malonda kuti adziikiza Ndalama za phindu la Malonda awo kuti achite bwino.
Mbusa Vincent Nguluwe, wapempha anthu kuti tiunguze pa zomwe sitinachite bwino ndipo tiphunzire pa zomwe tinaphonya mu 2024 ndikuchita bwino mu chaka cha 2025. Kuphatikizapo, Mbusayu wati amalawi tisakhale odalira zolandira kuchoka kwa anthu a Ndale ndipo tilape kuti tichite bwino.
Kusakonzekera ndi chimodzimodzi ndi kukonzekera kulephera.