MPHAMVU YA NYIMBO ZÀ KU MALAWI
Written by Kradio on February 8, 2025
Nyimbo ndi chinthu chimodzi chimene chimapezeka mnyengo zonse za munthu. Mkulu wa bungwe loyanga’anira oyimba mdziko muno la Musicians Union of Malawi ,Vita Chirwa, akufotokoza za momwe mayimbidwe akuyendera.
“Maimbidwe kuno kwathu ku Malawi, akupita patsogolo. Taona oyimba kuno kwathu akuitanidwa kupita kukayimba ku Mayiko akunja komanso kuwina photho za padziko lonse”. Vita wayamikira atsogoleri a kale a bungweli poika maziko abwino.
Iye wati ngakhale kuti momwe amabwera pa udindowu mchaka cha 2022, kubwera kwawo kudabutsa mpungwepungwe popeza anthu ena sanakhutire ndi momwe Masankho adayendera zomwe zidapangitsa kuti Chaka cha 2023 chonse chithe opanda ntchito yolozeka.
Bata litadza ku Bungweli(2024), Vita adakwaniritsa kupanga ubale ndi Sukulu ya ukachenjede wa Sayansi, ya MUST, kuti adzisinthana zochita kumbali ya Maimbidwe. Kuphatikiza apo , Bungweli lidalunga ndikuthandiza anthu omwe adakumana ndi Ngozi ya Namondwe Freddy ,pambali pa ma ubale ena.
Mkuluyu, wati Bungweli lawo lidalandira thandizo la ndalama kuchokera ku Copyright Fund ndi cholinga cholimbikitsa malingaliro a ngwiro pozindikira kupululuka kwa miyoyo ya anthu ongodzipha okha kaamba ka nkhawa.
Iye, wati izi zidachitika kutinso oyimba asamaimbe nyimbo zodandaulitsa.
Pankhani ya kagwiridwe ntchito ndi oyimba nyimbo za chikunja ndi za uzimu, Chirwa watsutsa mphekesera zokuti kumakhala kovuta kugwirira ntchito limodzi ndi ma guluwa.” Ku Musicians Union of Malawi, kulibe tsankho”. Watero, Vita.
Pa tanthauzo la oyimba kukhala kazembe ku bungwe kapena kampani, Vita Chirwa, wati izi zimatanthauza kuti woyimbayo wachita bwino pa Maimbidwe ake kuphatikizapo kuzitsatsa komanso ukadaulo.
Mkulu wa Bungwe la MUM-yu ,wati iye oyimbawa amamvetsetsa pa zomwe akuyenera kukwanilitsa akakhala Kazembe.
Kumbali ya kusakhutitsidwa kwa Kampani pa zochita za kazembe wake, Chirwa , wati pamakhara Mgwirizano ndipo bwalo la Milandu ndilomwe limathetsa kusamvanaku.
Luso la Makono kumbali yonyamulira uthenga wa Nyimbo, Vita Chirwa wati malo ngati YouTube pongotchulapo ochepa chabe ndi abwino popeza amathandizilanso kugulitsa oyimba.
Mkuluyu, wayamikiranso mabwalo oyimba kuti akumakhala abwino komanso anthu akumakhutitsidwa.
Pothirirapo ndemanga pa kuimba pa Msika wa dziko lonse, Chirwa wati izi zikutanthauza kuti ngati dziko tikusuntha ndipo walimbikitsa oyimba kuti adzibwera ndi photho za pamwamba za kunja (Grammy awards ).
Mtsogoleri wa Bungwe la anthu oyimbayu, wapempha anthu oyang’anira oyimba (managers) kuti asiye oyimba adzipanga za Nyimbo ndipo manager adzichita mbali yake ngati kusaka malo okaimbira.
Vita Chirwa, wathokoza ndi kuyamikira a Malawi kaamba ka chidwi ndi chithandizo chimene amapereka kwa oyimba kuno ku Malawi.
Bungwe la Musicians Union of Malawi (MUM), lidakhazikitsidwa mu 1994 ndipo lidalembetsedwa mwezi wa May ,mu 2002 ndicholinga choteteza ufulu ndi umoyo wa oyimba.