MALONDA A NYAMA YABWINO
Written by Kradio on February 25, 2025
Ngati muli pa Msika, tasuzumirani kumalo ogulitsira nyama kuphatikizapo nyama ya nkhuku. Mugwirizana nane kuti ndiwo ya nyama, ndiyokhayo yomwe imapangitsa phwando kapena mwambo wa Maliro kukhala osimbika. Nthawi zinanso angakhale ku Chilendo kumene akakuphikira nyama, umakhala ndi chimwemwe chodzala mtsaya. A James Simika ,omwe ndi mmodzi mwa anthu ochita Malonda ogulitsa nyama akusimba za malondawa.
” Timagulitsa mitundu yonse ya nyama ngati ; Nkhuku, Nyama yoperapera kuphatikizaponso Mang’ina.Chibwerereni panopa pa Gulliver (Area 49) mu mdzinda wa Lilongwe,anthu adatidziwa kuti pa Gulliver pamene pamakhala Nyama yabwino ndi pa Tower pano”. Simika, wafotokoza.
Mkuluyu ,wachenjeza anthu ochita Malonda a butchery kuti adzikhala osamalitsa komanso kusakhala ndi nkhawa iriyonse pamene ochita Malonda-wa akugwiritsa ntchito mpeni wa makono omwe umagwiritsa ntchito mphamvu ya magetsi podulira nyama mmiringo yosiyanasiyana.” Ndimakina (mpeni) owopsya. Ena adadukako dzala ndiye pamafunika kusamalitsa ukamagwiritsa ntchito Mpheni-wu, osatayirira”.
Kumbali ya kayendedwe ka malonda a nyama, James wadandaula kuti kugwa kwa mphamvu ya ndalama ya kwacha mwa kapitikapiti kwabwezeretsa malonda awo mbuyo. Mkulu ochita malonda-yu waulula kuti munthu thanks kukhala ndi Filiji zoonekera mkati, mpeni wa makono komanso ng’ombe imodzi akafuna kuyamba geni ya nyama.
Pa za mbiri yawo yogulitsa nyama yofewa, James waulula kuti nyama yawo amakagula ku Cold Storage, komanso amayisamalira bwino pamene magetsi athima poti ali ndi generator zothandizira kuziziritsa Nyama kupyolera mmagetsi ake. Simika, wagwirizana kwa thunthu ndi bungwe loona ndi kuyeza milingo ya zinthu mdziko muno la Malawi Bureau of Standards, kuti ukhondo umafunikira pa malonda omwe uli ndi kuthekera kokopa anthu ogula.
“Chipongwe kwa kasitomala, komanso bwana wako sizabwino kaamba koti zimakuika munthu mmavuto ochotsedwa ntchito”. Iye, wachenjeza. Simika, wati kasitomala amafunika kuchengetedwa ngati mwana komanso osamunyoza akabwera ndi ndalama yochepa.
James Simika, wamema anthu kuti adzigula nyama pa butchale yawo ya Fresh Food. Iye, wati amatha kumuotchera nyama kasitomala mwa ulere akagula nyama pa malowa. Mkuluyu waonjeezera kumema ochita malonda kuti alimbe mtima kuchita geni ngakhale katundu wakwera kwambiri pa msika.