Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

Author: Kradio

Page: 3

Nzosabisa kuti makono munthu ukafuna kupeza chinthu mosavuta kuchokera kwa adindo umayenera upereke Ndalama ya ‘fanta’. Izi zikapanda kuchitika zimakhala ngati tsiku si tsikunso. Dr. George Chaima, ati kubwera kwa ufulu okhala ndi zipani zambiri (demokalase) ,wakolezera mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu.”Kuyambira mchaka cha 1964 kufikira mchaka cha 1992,Malawi adali dziko lokoma. Munthu umatha kusiya […]

Kwa nthawi yaitali Ndale za dziko la Malawi zakhala ziri ndi nkhope za anthu akuluakulu. Lerolino achinyamata adzuka kutenga nawo gawo mu Ndale. Mkulu ochokera ku Generation 40,yemwenso amayankhulapo pa Nkhani zosiyanasiyana a Maloto Chimkombelo, avomereza kuti chiwerengero cha achinyamata omwe akuonetsa chidwi chofuna kusankhidwa mma udindo osiyanasiyana chachuluka.”Achinyamata ambiri akuonetsa chidwi  chochita misonkhano yokopa […]

Pamene zipani za Ndale zosiyanasiyana ziri kalikiriki kuchititsa misonkhano yosankha adindo(convention) omwe adzaimirire pa chisankho cha mchaka cha mawa, mmodzi mwa akuluakulu oyankhulapo pa nkhani za achinyamata mdziko muno a Davis Damison ,amema achinyamata kuti adzatenge nawo gawo pa Masankho a mchaka cha 2025 kuti akwaniritse kufikira zinthu zomwe amazifuna pokhala ndi adindo akumtima kwawo. […]

Nzosabisa kuti kwa nthawi yaitali achinyamata amauzidwa kuti ndi atsogoleri a mawa ,koma izi siziri chomwechi popeza katswiri pa Ndale mdziko muno a George Phiri, wati achinyamata ndi atsogoleri a lero.”Achinyamata tisamawanamize kuti adzakhala atsogoleri a mawa ayi. Tiyeni tisinthe ka ganizidwe ndipo ndibwino kuti achinyamta-wa apatsidwe mpata otsogolera lero. Wachinyamata ndi wachinyamata lero”. Malingana […]

The research by Mwapata Institute and  the National Youth Council of Malawi themed “Prospects and Barriers to Youth Engagement in Agriculture and Food Systems in Malawi” has massively  exposed a decline in youth engagement in agricultural activities across the country. The report highlights lack of resources like land and steady market and knowledge deficiency as […]

Zakudya, mavalidwe ,Nyimbo ndi Miyambo ndi zina mwa mbendera zomwe zimaulula za Chikhalidwe cha munthu. Makono dziko lapansi likuyenda ngati mudzi umodzi kaamba ka chitukuko chogwiritsa ntchito makina monga Lamya ndi ma Kompiyuta. Mfumu yaikulu Lukwa ya M’boma la Kasungu yadandaula  kuti a Malawi ataya Chinkhalidwe chawo potengeka ndi zochitika zomwe amawona Mmaiko ena.”Dziko la […]

Mukayenda mmakwalala,nzikhuthe ,malo ochitira ma sewero osiyanasiyana ndi kwina komwe achinyamata amasonkhana mupeza kuti pakati pawo pamakhala chikoka cha kugawana zakumwa ndi Fodya . Zambiri mwa izo  zimakhala Mankhwala ozunguza ubongo. Katswiri pa thanzi la kaganizidwe ka ngwiro a Joseph Maseke, ati Mankhwala ozunguza ubongo ndi Mankhwala omwe mkati mwake muli zinthu zosokoneza ubongo. “Pali […]

Mkhalakale pa Ndale a Jessey Kabwira ,apempha Bungwe lothana ndi Katangale ndi Ziphuphu la ACB,kuti lichitepo kanthu pofufuza ndi kupereka chilango kwa anthu omwe amachita katangale ponena kuti dzikoli likunyeka pa moto kaamba ka mchitidwe wu. Kabwira wati mdani wa mkulu wa utsogoleri wabwino ndi kudzikonda komwe kumachititsa kuti atsogeri azidzikundikira chuma. Utsogoleri umayenera kuimira […]

Pamene ngozi zagwa mwadzidzidzi anthu amakhala kakasi kusowa mtengo ogwira, izi ndi kutsatira kusakhala ndi ishulansi pa moyo wamunthu kapena katundu. Imodzi mwa bank yochita zinthu zake mwa makono ya Centenary, ili kalikiliki gugulitsa insurance kuti anthu asamatuluke thukuta zovuta zikaagwera. Mkulu oyanganira ntchito za Bank-assurance ku Centenary bank a James Akuseka Msiska , wati […]

Mneneri mu nthambi ya unduna wa zokopa alendo ndi zachirengedwe, a Joseph Nkosi ati dziko la Malawi likupita patsogolo potukula ntchito yosamalrira malo osungira Nyama za kutchire ndi zachirengedwe zomwe ziri ndi kuthekera kotukula dziko lino pa Chuma. Polankhula mu Program ya “Touring Malawi”  pa wailesi ya Kasupe , a Nkosi afotokoza kuti malo osungira […]


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist