Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

Blog

Chuma ndi chinthu chimene chimafunikira kwambiri pa moyo wa munthu aliyense posatengera komwe  munthu amachokera. Maphunziro a nkhani za chuma kuno kwathu ndi mnyanga wa njobvu. Katswiri pa nkhani ya zachuma,Innocent Banda watsindika kuti  muli phindu mma phunziro a nkhani za chuma”Maphunziro a zachuma ali ndi  phindu pa munthu payekha chifukwa Ndalama-zo amazipeza ndi munthu”. […]

Mawu akuti bongololo sadzolera mafuta pa gulu akugwirizana kwambiri ndi zomwe zipani za ndale zimachita pa nkhani youlula komwe kumachokera chuma chake. Victor Chipofya, yemwe ndi katswiri pa nkhani za ndale wati  aMalawi samamvetsetsa momwe ndalama zoyendetsera zipani zimachokera.”Nthawi zambiri Chipani chokuti chiri kotsutsa chikangolowa m’boma chimayamba kugula magalimoto ankhaninkhani.Izi zimadabwitsa kuti ndalama azitenga kuti?.Nchifukwa […]

Zovala zomwe anthu timavala zimagwirizana ndi nyengo, ntchito zathu zimene zimachitika malingana ndi Nyengo. Tikawunikira nyengo ya mvula  kuno kwathu ku Malawi ,nayo idasintha. Chifundo Dalireni , yemwe  ndi mmodzi mwa akatakwe a zachirengedwe watsimikiza kuti nyengo idasintha.”Nyengo idasintha pafupifupi pa dziko lonse lapansi”. Katswiriyu wafotokoza kuti kudula mitengo, kutulutsa utsi kwambiri ku  ma fakitale […]

Malo ogwirira ntchito ali ngati  nyambo mmanja mwa mnsodzi ndipo kugwira ntchito kumayika chimwemwe mtsaya pomwe malipiro akuperekedwa.Komatu kuzindikira ntchito yako  nkofunika pa Kampani kapena bungwe  limene munthu akuligwirira ntchito. Mkulu ochokera ku Bungwe lolimbikitsa luso  losiyanasiyana pakati pa achinyamata la CISE Malawi, a Davis Damison, wafotokoza kuti  ndikofunikira kwambiri  ngati bungwe kapena kampani  kudziwa […]

Mutha kuvomerezana nane kuti  mwasiya kaye zimene mumachita ndipo mukuwerenga nkhani iyiyi. Mukamaliza, muzikonzekeretsa kuchita zinthu zina. Izi ndi chimodzimodzi ndi kuzikonzekeretsa mmoyo omwe mungakhale mutapuma pa ntchito kapena  bizinezi. Benard Chiluzi, mphunzitsi wa kayendetsedwe kabwino ka chuma  kuchokera ku old mutual, wadandaulira a Malawi  kuti adzikhala akuikiza ndalama  ngati njira imodzi  yozikonzekeretsa kupuma pa […]

Zamoyo zirizonse zimayenera kulandira chakudya cha bwino  kuti zidzikula ndi thanzi. Nayo mbewu ndi chimodzi mwa zinthu za Moyo zomwe zimafuna zakudya zabwino.A Tyson Chapuma, yemwe ndi Mlangizi pa nkhani za Ulimi ku Lunyangwa  research station  m’boma la Mzuzu , wati akugwira ntchito  usiku ndi usana kufufuza za chakudya cha mbewu mu nthaka. Pothirirapo mulomo […]

Next Level Academy, a renowned initiative from the United States of America , has praised Malawi for making significant strides in the creative arts industry. The sentiments were shared by MeccaGodZilla, the team leader for Next Level Academy, during a 10-day masterclass and workshop being held in Lilongwe. The workshop is designed to provide intensive […]

Nyimbo ndi chinthu chokhacho chimene chimathuzitsa mtima pamene munthu ali m’chisoni, kukuza chimwemwe kwa munthu amene ali mchisangalalo komanso kuthandizira kugwira ntchito  mosafooka. Gulu la Peace  Soldiers  , lomwe limayimba chamba cha Reggae, lati lidabadwa mu chaka cha 2003 ndi cholinga chofuna kupeza njira  pa  kulankhula pa zomwe gululi linkadana nazo ku Sukulu ya Secondary. […]

Pa zinthu zomwe munthu amaganizira tsiku ndi tsiku ndalama  imakhala pa mndandanda wa zinthu zoganiziridwa. Kaganizidwe kangwiro nako ndi kofunikira pa nkhani ya ndalama. Benard  ChiluzI, yemwe ndi Mkulu oyang’ana za maphunziro abwino a kayendetsedwe ka chuma ,wati kuganiza molungama ndi kaganizidwe komwe sikungamupezetse munthu mavuto kapena ndi kuganiza mu njira ina chifukwa cha zinthu […]

Litsiro ndi chinthu chokhacho chimene tsiku lake lobadwa silimadziwika ndipo limaberekana mwa kathithi. Mthupi mwa munthu namo mumakhala litsiro. Namkungwi pa nkhani ya zakudya,  Gladys Bandawe ,kuchokera ku Hope nutrition Services, watutumutsa mtundu wa a Malawi ponena kuti mthupi mwa munthu mumakhala litsiro.” Mkati mwathupi mumakhala litsiro limene limafunika kutsuka chimodzimodzi   limene limakhala kunja kwa […]


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist