Blog
Page: 2
Zamoyo zirizonse zimayenera kulandira chakudya cha bwino kuti zidzikula ndi thanzi. Nayo mbewu ndi chimodzi mwa zinthu za Moyo zomwe zimafuna zakudya zabwino.A Tyson Chapuma, yemwe ndi Mlangizi pa nkhani za Ulimi ku Lunyangwa research station m’boma la Mzuzu , wati akugwira ntchito usiku ndi usana kufufuza za chakudya cha mbewu mu nthaka. Pothirirapo mulomo […]
Next Level Academy, a renowned initiative from the United States of America , has praised Malawi for making significant strides in the creative arts industry. The sentiments were shared by MeccaGodZilla, the team leader for Next Level Academy, during a 10-day masterclass and workshop being held in Lilongwe. The workshop is designed to provide intensive […]
Nyimbo ndi chinthu chokhacho chimene chimathuzitsa mtima pamene munthu ali m’chisoni, kukuza chimwemwe kwa munthu amene ali mchisangalalo komanso kuthandizira kugwira ntchito mosafooka. Gulu la Peace Soldiers , lomwe limayimba chamba cha Reggae, lati lidabadwa mu chaka cha 2003 ndi cholinga chofuna kupeza njira pa kulankhula pa zomwe gululi linkadana nazo ku Sukulu ya Secondary. […]
Pa zinthu zomwe munthu amaganizira tsiku ndi tsiku ndalama imakhala pa mndandanda wa zinthu zoganiziridwa. Kaganizidwe kangwiro nako ndi kofunikira pa nkhani ya ndalama. Benard ChiluzI, yemwe ndi Mkulu oyang’ana za maphunziro abwino a kayendetsedwe ka chuma ,wati kuganiza molungama ndi kaganizidwe komwe sikungamupezetse munthu mavuto kapena ndi kuganiza mu njira ina chifukwa cha zinthu […]
Litsiro ndi chinthu chokhacho chimene tsiku lake lobadwa silimadziwika ndipo limaberekana mwa kathithi. Mthupi mwa munthu namo mumakhala litsiro. Namkungwi pa nkhani ya zakudya, Gladys Bandawe ,kuchokera ku Hope nutrition Services, watutumutsa mtundu wa a Malawi ponena kuti mthupi mwa munthu mumakhala litsiro.” Mkati mwathupi mumakhala litsiro limene limafunika kutsuka chimodzimodzi limene limakhala kunja kwa […]
Pa miringo ya zinthu zomwe zimalingidwa pali mulingo umodzi wokha umene umapereka mafunso ngati kalingidwe kakusemba ndondomeko maka olingayo akakhala wa mamuna ndipo akulinga munthu wa mkazi. Chovala , ndi chithu chokhacho chomwe chimalingidwa ndi mmisiri wosoka. Thomson Geza, Yemwe ndi mmodzi mwa wosoka zovala ku msika wa Galliver mu mzinda wa Lilongwe, wavomereza kuti […]
Kusowa kwa maphunziro a za Chuma pakati pa a Malawi kuli ngati kusowa kwa Chipatso cha Mpinjipinji Mnkhalango za dziko lino.Katswiri pa nkhani za Chuma a Innocent Banda, watsindika kuti ma Phunziro a za Chuma ndi osowa ngakhale ali ofunika. “Maphunziro a za chuma ndi ofunika chifukwa ndi chimene chimapereka mphamvu kwa anthu pothetsa umphawi,kutukula […]
Ndizosabisa kunena kuti Moto wa khala la Mtengo wa Tsanya omwe umayaka ku Bungwe lothana ndi Katangale ndi Ziphuphu tsopano uli ngati Moto wa Mapesi. Katswiri woyankhulapo pa nkhani za Utsogoleri wabwino komanso momwe zinthu zikuyendera mdziko muno Victor Chipofya, wati sakumva nkhani mma Nyuzipepala ngati momwe zinaliri mbuyomu .”Sitikumva zinthu mma Nyuzipepala ngati mmene […]
Mdima wa ndiwe yani wokhudza zomwe zidachitika kuti ndege yomwe idanyamula wachiwiri wa kale wa Mtsogoleri wa dziko lino Malemu Dr Saulosi Klaus Chilima , udakakodolabe Mitsinje ya misonzi kwa a Mary Chilima ,omwe pa 29 September 2024 adalemba pa tsamba la mchezo la facebook kupempha okhuzidwa onse kuti awathandize kupanga kafukufuku wapadera. Iwo adajambulitsa […]
Mkuluwiko wokuti zingalume phula n’tenga ndi nkuluwiko omwe wamangirira uthenga omwe Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazalus Chakwera, anali nawo kwa mamulumuzana a Bungwe la mgwirizano wa Maiko apa dziko lonse lapansi. Mmodzi mwa akatswiri omwe amayankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana mdziko muno a Dr George Chaima , ayamikira Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera […]