MARY CHILIMA WAPEMPHA KAFUKUFUKU WAPADERA
Written by Kradio on October 4, 2024
Mdima wa ndiwe yani wokhudza zomwe zidachitika kuti ndege yomwe idanyamula wachiwiri wa kale wa Mtsogoleri wa dziko lino Malemu Dr Saulosi Klaus Chilima , udakakodolabe Mitsinje ya misonzi kwa a Mary Chilima ,omwe pa 29 September 2024 adalemba pa tsamba la mchezo la facebook kupempha okhuzidwa onse kuti awathandize kupanga kafukufuku wapadera. Iwo adajambulitsa pa malo pomwe ndenge yomwe idanyamula amuna awo idagwera pamene amakumbukira ulendo wawo wa banja ndi Malemuwa . Mayi Mary Chilima ,apempha a Malawi kuti pakhazikitsidwe bungwe lomwe lichite kauniuni pa zomwe zidachitika mwatsatane tsatane kuchoka pa 10 june kufika pa 11 june tsiku limene ndege idapezeka kuti yagwa.
Katswiri woyankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana a George Phiri , wayikira kumbuyo ganizoli ponena kuti ndizoyenera kutero. “kwa ineyo ndikuona kuti ndi choyenera chifukwa chichitikireni ngozi ija kafukufuku amene wachitika sadaonetse chomwe chidachitika kuti ndege igwe komanso anthu onse afe. A Malawi komanso mkazi wa Malemu Saulos Chilima akuyenera kudziwa chomwe chidachitika kwa a Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu ”. Phiri, watero.
A George Phiri ,apempha Boma kuti likuyenera kukhazikitsa kafukufuku wapadera woyima payekha (independent commission of Inquiry) kuti akubanja ndiye adzalengeze zotsatira za kafukufuku yu. A Phiri avomereza kuti a Mary Chilima sali okhutitsidwa ndi kafukufuku yemwe wachitikapo kale ndi gulu la akatswiri owona zangozi ya Ndege la ku Germany, la German Federal Bureau of Aircraft Accident Investigation . ” Ngati a Malawi sakumvetsa za zimene zidachitika ku Chikangawa , nawo a Mary sakumvetsetsa kuti vuto la Ndege linali lotani chifukwa Ndege siidapse, chidachitika ndi chani kuti anthu adzikasaka ndege komwe siidagwere?”. Phiri watero akudabwa.
Phiri watsindika kuti Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ,wachedwa kukhazikitsa kafukufuku wapadera.” Tikhoza kunena kuti Mtsogoleri wadziko lino wachedwa pamene padutsa miyezi itatu asadakhazikitse kafukufuku mpakana pano chigwereni ndege. Ngakhale Mtsogoleri wa dziko lino sadapite pa malo omwe adachitikira Ngozi ya ndege,zikuonetseratu kuti alibe chidwi”. Komabe mkuluyu wati ngakhale kafukufuku angakhazikitsidwe pakhale kusintha kuti zomwe kafukufuku apeze akhale ndi phindu. Iye anapitiriza kunena kuti Boma lisamakhalire zinthu za kafukufuku wapadera.
A George Phiri , avomereza kuti ndale zimalowerera pa kafukufuku.” Ndale zimalowererapo chifukwa amakhazikitsa kafukufuku ameneyu ndi atsogoleri a ndale omwenso amalandira lipoti ndi kulengeza zotsatira za kafukufuku”. Mkuluyu wati akubanja , asilikali ndi anthu ena okhudzidwa asakhale mu gulu lomwe lichite kafukufuku kuti zotsatira zake zidzakhale zovomerezeka.
Phiri wamema a Malawi kuti aphunzire kumafunsa atsogoleri pa zinthu ngati zimenezi ndipo ngati pangakhale kunyalanyaza njira zina zikhalepo kuti amene wakhalira lipoti adzibweza Ndalama zonse zomwe zagwiritsidwa ntchito pochitira kafukufuku.
Pa 10 June 2024,Dziko la Malawi lidachita tsembwe ndi kusowa kwa ndege ya a silikali yomwe idanyamula wachiwiri wakale wa Mtsogoleri wa dziko lino yemwenso adali Mtsogoleri wa Chipani cha United Transformation Movement (UTM) ndi anthu ena asanu ndi atatu. Ndege yi idapezeka mu nkhalango Ya Chikangawa M’boma la Mzimba
Dr Saulos Klaus Chilima adali katswiri pa nkhani za Chuma komanso wa ndale yemwe adakhalapo ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino kuchokera mchaka cha 2014 kufikira 2019 komanso 2020 kufikira nthawi ya imfa yawo mu 2024.