Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist

Author: Kradio

Kusowa kwa maphunziro a za Chuma  pakati pa a Malawi  kuli ngati kusowa kwa  Chipatso cha Mpinjipinji Mnkhalango za dziko lino.Katswiri pa nkhani za Chuma a Innocent Banda, watsindika kuti ma Phunziro a za Chuma ndi osowa ngakhale ali ofunika. “Maphunziro a za chuma ndi ofunika chifukwa ndi chimene chimapereka mphamvu kwa anthu pothetsa umphawi,kutukula […]

Ndizosabisa kunena kuti Moto wa khala la Mtengo wa Tsanya omwe umayaka ku Bungwe lothana ndi Katangale ndi Ziphuphu  tsopano uli ngati Moto wa Mapesi. Katswiri woyankhulapo pa nkhani za Utsogoleri wabwino komanso momwe zinthu zikuyendera mdziko muno   Victor  Chipofya, wati sakumva nkhani  mma Nyuzipepala  ngati momwe zinaliri mbuyomu .”Sitikumva zinthu mma Nyuzipepala ngati mmene […]

Galimoto za mtidzi, nyumba za pamwamba  komanso zovala zodula  ndi zina mwa zinthu zomwe mtima umafuna utazipeza mmoyowu.Ichi chifukwa  chake pali mkuluwiko wotchedwa ‘mtima Suvala Sanza’. Davis Damison yemwe ndi mkulu wa Community Initiative for Social Empowerment (CISE)Malawi , wafotokoza kuti kauniuni wa Moyo (life style audit)ndi makhalidwe  a munthu potengera zinthu zimene wapeza kapena […]

Mdima wa ndiwe yani  wokhudza zomwe zidachitika kuti ndege yomwe idanyamula wachiwiri wa kale wa  Mtsogoleri wa dziko lino Malemu Dr Saulosi Klaus Chilima , udakakodolabe Mitsinje ya misonzi kwa a Mary Chilima ,omwe  pa 29 September 2024  adalemba pa tsamba la mchezo la facebook  kupempha  okhuzidwa onse kuti awathandize kupanga kafukufuku wapadera. Iwo adajambulitsa  […]

Mkuluwiko wokuti zingalume phula n’tenga ndi nkuluwiko omwe wamangirira  uthenga omwe Mtsogoleri wa dziko lino  Dr Lazalus Chakwera,  anali nawo kwa mamulumuzana a Bungwe la mgwirizano wa Maiko  apa dziko lonse lapansi. Mmodzi mwa akatswiri omwe amayankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana mdziko muno a Dr George Chaima , ayamikira Mtsogoleri wa dziko lino  Dr Lazarus Chakwera […]

A baseline survey conducted by RBM in 2014 revealed that only 17% of adults utilized formal financial services, while a significant 53% relied on informal options. This gap is largely attributed to a lack of understanding of formal financial products, reflected in a concerning financial literacy index of just 3.6%. RBM Governor Wilson Banda emphasized […]

Sabata silimatha anthu okhala Mmizinda ndi mma town a Dziko lino asadaone zibinyira za zinyalala mphepete mwa Misewu zikudikira kunyamulidwa kuti zipite ku Mtaya. A Stephen Chiunjira ndi nkulu wa  Bungwe la Our World international ,yomwe imapanga zosintha zinyalala kuti zikhale Manyowa ndi zinthu zina zosiyanasiyana ku Kawale 2, mu Mzinda wa Lilongwe . Iwo […]

Kwa nthawi yaitali anthu mdziko muno akhala akututumuka ndi imfa zokudza  pongodzipha.A Joseph Maseke, katswiri pa nkhani yoona za thanzi la mmalingaliro watambasula kuti kaganizidwe ka ngwiro ndi kukhala osakhumudwa kapena nkhawa mmalingaliro. A Maseke atchula  ma ubwenzi amene achinyamata amakhala nawo kuti ali ndi kuthekera kwa kukulu kokhudza kaganizidwe ka ngwiro. Katswiri-yu wadandaula  kuti […]

Munthu umafika ponyasitsa nkhope pamene maso ako akumanizana ndi zinyalala mmizinda ndi mma town a dziko lino.Bungwe la Clean Cities Project lidabadwa ndi cholinga chofuna kulimbikitsa  kusamalira chirengedwe, kusintha kwa Nyengo ndi ukhondo. Mtsogoleri wa Bungwe-li, Martin Manyozo  wati  iwo monga achinyamata ndi anthu okonda dziko lino kotero kuti  akufuna kuthandizira kusintha mizinda yathu malingana […]

Recent developments in Malawi’s efforts to combat hunger have sparked a range of reactions from agricultural experts, Members of Parliament, and other stakeholders. The government’s announcement of maize distribution has become a contentious issue, with varying opinions on the fairness and effectiveness of the allocation of maize. Minister of Agriculture, Sam Kawale recently revealed in […]


Kasupe Radio Live

Kasupe Radio Live

Current track

Title

Artist